Project Hope     home >>stonecroft>> mayendedwe otsogolera
Stonecroft - Mayendedwe Otsogolera
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mayendedwe Otsogolera

Cholinga

Kufikira — Zophunzirazi zimathandizira kupereka njira zopindulitsa pa kufalitsa uthenga wa chipulumutso chodzera mwa Yesu Khristu kwa wena. Iwo amene ali mu gulu alikulumbikitsidwa kuitana anzao, a mubanja lawo, ogwira ntchito nao limodzi ndi iwo amene amakhala nawo khomo loyandikana.

Kupanga maphunziro aophunzira —Obadwa kumene mwatsopano ndi a Khristu okhwima atha kuphunzira za mbiri za Mulungu ndi kukula mu ubale ndi Iye. Maphunzirowa amafotokoza za m'mene ungagwiiritsire malemba pa nyengo za tsiku ndi tsiku.

Kusiyana

Chimene chimapangitsa maphunziro a Baibulo a Stonecroft kukhala osiyana ndi ina onse ndi chani?

• Uthenga wabwino Chipangano cha Tsopano — Maphunzirowa apangidwa kuti agwiritsidwe ntchito ndi Chipangano cha Tsopano chifukwa matsamba ake apangidwa kuti kupeza mau ena mbaibulo kusakhale kovuta. (Manambala a matsamba ndi olingana ndi GoodNews4th Edition Chipangano cha tsopano) Baibulo la GoodNews ndilovomerezeka ndi mipingo ya mbiri.

• Maphunzirowa alembedwa mu njira yosavuta kugwiritsa ntchito kwa iwo amene akuyamba kumene maphunziro a Baibulo pa dziko lonse la pansi.

• Buku lotsogolera ndi longothandizira, koma si mphunzitsi.

Njira

Maphunziro a Baibulo a Stonecroft ndi osavuta kuwerenga.

Zounikira mu buku lotsogolera zili m'malire. sizikuyenera kuwerengedwa mokweza. Mau olembedwa mu bokosi alinso mu buku lophunzirira. Izi zikuyenera kuwerengedwa mokweza ndi iwo amene akuchita nawo maphunziro a Baibulowa.

Ndandanda wa madontho (. . . . .) umasonyeza kuti buku lotsogolera limalola gulu kuti litenge nawo mbali pakuyankha funso, kuwerenga vesi la m'Baibulo ndi kukambirana za phunziroli.

Malembo akuluakulu a mBaibulo, otsatana ndi madontho asanu , akuyimira vesi imene ikuyenera kuwerengedwa mokweza ndi m'modzi mwa anthu a pa gulu lanu pamene mukuphunzira. Pamene zosonyezera ma lemba a m'Baibulo zalembedwa m'malembedwe olembedwa nthawi zonse, zikuthanthauza kuti ndi zazitali kwambiri kuti ziwerengedwe pa gulu kapena ndizosafunikira kuti mungapezeko yankho.

Musadayambe Kuphunzira

Zofunikira—

• Khalani obvomerezeka ngati Otsogolera Stonecroft pakutsiriza ndondomeko yolembera maphunziro a baibulo.

• Phunzirani cholinga, chindunji, ndi mdandanda wa maphunziro.

• Tengani zipangizo zophunzirira za maphunziro anu ku Stonecroft Ministries-(800) 525-8627.

• Zophunzira zofunikira pa maphunzirowa:

* Mabuku ophunzirira

* Mabuku otsogolera

* Baibulo or the Africa Bible Verse Handbook for students that do not have their own Bible

* Ukhulupirira? Mabuku ang'onoang'ono a iwo amene akufunsa m'nene angalandirire Yesu ngati mpulumutsi.

* Makadi a uthenga

• Pezani malo oyenerera ochitira maphunziro anu. Ganizirani zochitira maphunziro anu mu nyumba, malo ogwirira ntchito, malo odyera, malo ochezera, malo ogulitsira khofi, ndi ena ambiri.

Konzekerani ma phunziro anu—

• Malizani maphunziro pakulemba mu buku lophunzirira musanawerenge buku lotsogolera. Izi zikuthandizani kuti kuti mumvetse maganizo a wena kuti mumvetse mayankho awo.

• Phunzirani kuwerenga maphunziro mokweza, ngati ndikotheka. Lembani nzere kunsi kwa liwu kapena chiganizo chofunika zimene zikuthandizireni popereka phunziro ku gulu. Ganizirani nthawi imene muifune powerenga mau kuti mudziwe nthawi imene mungafune pokambirana.

• Tsimikizirani malo, nthawi, ndi chisamaliro cha mwana, ngati ndikofunika.

• Pemphererani iwo amene akudzakhala nawo pa maphunziro a Baibulowo.

Pophunzira mau a Mulungu

Gawani mabuku ophunzirira ndi Chipangano cha Tsopano ndipo mutolele malipiro. Sonkhani ndalama za pokhalira mwana, ngati nkoyenera. Tolelani malipiro ndipo ndipo bwezani zipangizo zina zapadela mwansanga.

Yambani phunziro ndi pemphero. Ngati wina anena chofunika kupempherera, gulu lilembe pa malo olembapo zopempherera ku mbuyo kwa buku lophunzirira ngati chikumbutso choti chipemphereredwe sabata imeneyo. Ngati chopempherelacho ndi chofunika mwa nsanga, chipempherereni potsegula ndi pemphero.

Kumbukirani, pakukumana koyamba munthu aliyense adzalemba yankho lake mu buku lophunzirira pamene mukuphunzira. Limbikitsani gulu kuwerenga phunziro musanakumane kuti mukumbukire pophunzira.

Werengani ndipo mupereke uthenga mu buku lotsogolera mokambirana, pamene mukuyang'anana.

Werengani ndi ku phunzirani ndi gulu lonse; simukufunika kukhala katswiri wa Baibulo.
Buku lotsogolera limaika lokha ndondomeko pa:

• Nthawi yoyamba ndi kutsiriza.

• Kugwiritsa ntchito buku lotsogolera ndi Baibulo ngati zothandizira. Palibe china choonjezera chimene chimafunika.

• Limbikitsani wina aliyense kuti atengepo mbali ndipo muonetsetse kuti palibe wina amene akutenga mbali yayikulu pa kulankhula kwambiri kuposa anzake.

• Pangani maphunzirowa kukhala olunjika pa Yesu Khristu, osati pa za chiphunzitso cha mpingo, za ndale, kapena za moyo wa padziko. (DZIWANI: pa za maphunziro a m'matchalitchi, mafunso a ziphunzitso za mpingo amayankhidwa mu njira zina.)

Yanganani mu gulu mwanu amene angapange zotsogolera zabwino pa maphunziro akutsogolo.

Ngati otsogolera, khalani chitsanzo chosonyeza nzeru ndi kuganiza kwa bwino poyankhula. Letsani anthu kuyankhula zinthu zimene zizikuyenera kulankhulidwa pa gulu. Pambali pa gulu, pempherani nawo ndipo alimbikitseni afufuze uphungu wa uMulungu oyenerera.

Funsani ophunzirawo kuti aganize za anthu amene angathe kuwaitana kumaphunziro ena. Alimbikitseni kuti ayambe kupempherera wina ndi mzake potchula ma ina awo.

Zokumbutsa Zofunika

• Ngati simutha kutsogolera maphunziro pa chifukwa chilichonse, munthu ovomerezeka ndi wophunzitsidwa akuyenera kulowa m'malo mwanu.

• Mukafuna kudziwa za mbiri zokhudzana ndi ndomdomeko, zipangizo zophunzirira, kapena m'mene mungachitire, funsani ku Stonecroft Bible Studies pa (800) 525-8627. Email connections@stonecroft.org

“Khalani a tcheru, imani molimba mu chikhulupiriro, khalani olimba mtima, khalani amphamvu. Chitani ntchito zanu zonse mwa chikondi.”

—1 Akorinto 16:13-14

Atsogoleri amatsogolera

 
 

 

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us