Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani?
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

Losimdikizidwa ndi Utumiki wa Stonecroft
P.O. Box 9609, Kansas City, MO 64134-0609

Chiyambi

KODI MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?
KODI MUNADABWAPO?

Baibulo limatiuza kuti Mulungu wakhala aliko ndipo adzakhalako mpaka muyaya. Ndiye olenga moyo ndi kupereka zonse zofunikira za moyo. Mulungu ndi Mzimu. Ndi wa Ulemelero, ndi wamphamvu zonse, ndi woyera, wokhulupirika komanso wachilungamo.
Mulungu ndi wosamvetsetseka komatu titha kudziwa za Mulungu amene sitimdziwayo. Kodi mumamudziwitsitsa Mulungu? Cholinga cha moyowu ndi kumudziwa Mulungu. Tinalengedwa kuti timdziwe ndi kumkweza. Choncho kukhala osadalira Mulungu tidzinyenga tokha.

Mulungu akudalitseni pamene ndi pemphero mukuphunzira ndi kumudziwa Mulunguyo mwa inu nokha.

Pakuti atero Yehova—

Amene analenga kumwamba;
Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi;
Nalipanga:
Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe: Iye analiumba akhalemo anthu, —
“Ine ndine Yehova, Ndipo palibenso wina.”

—Yesaya 45:18

Lucille Fern Sollenberger

Ndondomeko yophunzilira

Maphunziro awa ndi mawu a Mulungu omwe cholinga chenicheni ndi kuphunzira zimene baibulo likunena komanso limakhudza bwanji miyoyo yathu. Buku lophunzilira komanso Baibulo ndi zida zokhazo zimene tigwiritse ntchito pamaphunzirowa.

Poyamba tiyankhe kaye mafunso amene ali mu mabuku ophunzilira tisanayambe phunziro liri lonse. Iyi ndi njira yokonzekera phunziro liri lonse zomwenso zipangitse kumvetsa kwa kukambirana kwathu. Tipanga phunziro loyamba limodzi. Maphuzirowa ayamba munthawi yoyikika ndikutha pakati pa ola limodzi ndi ola limodzi ndi theka.

Pakuti tikusiyana kochokera kuphatikizapo matchalichi timverana ndi kulemekeza maganizo ngakhalenso zikhulupiliro za aliyense.

Mmasabata ochepa akudzawa. Tikufuna tiyambe maphunziro atsopano a baibulo kuchokera ku bungwe la Stonecroft. Ganizirani anzanu amene mungawayitanire maphunzirowa.

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 

 
 

 

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us