Project Hope     home >>stonecroft>> >> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1 >> phunziro 2
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 2
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mavesi a m'Baibulo

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

1 Akorinto 1: 9
9Mulungu ali, wokhulupirika amene munaitanidwa mwa iye, ku ciyanjano ca Mwana wace Yesu Kristu, Ambuye wathu.

Aroma 16:27
27kwa Mulungu wanzeru Yekha Yekha, mwa Yesu Kristu, kwa Yemweyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

Luka 1:37
37Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

Yohane 3:16
16Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

Numeri 23:19
19Mulungu sindiye munthu, kuti aname; Kapena mwana wa munthu, kuti aleke; Kodi anena, osacita?

Cibvumbulutso 15: 3-4
3Ndipo ayimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Nchito zanu nzazikuru ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. 4Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

Cibvumbulutso 1: 8
8Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

Akolose 1: 15-16
15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse; 16pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.

Funso #2

Yohane 4:24
24Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'coonadi.

Mulungu wathu ndi Zopanda Malire

1 Mafumu 8 : 27
27Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m'Mwambamwamba zicepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

Yobu 11 : 7-9
7Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna?
Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?
8Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungacitenji?
Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?
9Muyeso wace utalikira utali wace wa dziko lapansi,
Citando cace ciposa ca nyanja.

Mulungu sitingathe kuzimvetsa

Yobu 37 : 5
5Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ace, acita zazikuru osazidziwa ife.

Isaiah 55 : 8-9
8Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati Yehova. 9Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitari kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

Aroma 11 : 33-36
33Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace kwa Mulungu! 4 Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka! 34Pakuti 5 anadziwitsa ndani mtima wace wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wace ndani? 35Ndipo 6 anayamba ndani kumpatsa iye, ndipo adzambwezeranso? 36Cifukwa 7 zinthu zonse zicokera kwa iye, zicitika mwa iye, ndi kufikira kwa iye. 8 K wa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

Funso #3

1 Yohane 4: 8
8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.

2 Atesalonika 3: 3
3Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

Yakobo 1:17
17Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko, kapena mthunzi wa citembenukiro.

Marko 10:18
18Ndipo Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.

Ahebri 1: 8
8Koma ponena za Mwana, ati,
Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

Luka 1:78
78Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.
M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;

1 Petro 1: 15-16
15komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; 16popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

Malingaliro a Mulungu

Mulungu ndiye chikondi

1 Yohane 4: 7-16
7Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu, 8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi. 9Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.
10Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu. 11Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo 12Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife; 13m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace. 14Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu. 16Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.

Aefeso 2: 4-5
4koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco, 5tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),

Mulungu ndi wokhulupirika

Deuteronomo 7: 9
9Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.

Masalmo 92: 1-2
1Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu: 2Kuonetsera cifundo canu mamawa, Ndi cikhulupiriko canu usiku uli wonse.

Mulungu sasintha

Malaki 3: 6
6Pakuti Ine Yehova sindisinthika, cifukwa cace inu ana a Yakobo simunathedwa.

Mulungu ndi wabwino

Masalmo 107: 1
1Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.

Mulungu basi

Deuteronomo 32: 4
4Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro; Pakuti njira zace zonse ndi ciweruzo;
Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika,

Mulungu ndi wachifundo

2 Akorinto 1: 3
3Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,

Mulungu ndi woyera

1 Samueli 2: 2
2Palibe wina woyera ngati Yehova; Palibe wina koma Inu nokha; Palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

Masalmo 99: 9
9Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, Ndipo gwadirani pa phiri lace loyera;
Pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.

Funso #4

1 Petro 1: 13-16
13Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu m'bvumbulutso la Yesu Kristu; 14monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; 15komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; 16popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

1 Akorinto 1:30
30Koma kwa iye muli inu mwa Kristu Yesu, 7 amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi cilungamo ndi ciyeretso ndi ciombolo;

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us