Project Hope     home >>stonecroft>> >> mavesi a m'baibulo >> phunziro 4 >> phunziro 5
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 5
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mavesi a m'Baibulo

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Yeremiya 29:13
13Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

Yohane 14: 21-23
21Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye. 22Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? 23Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

Aroma 5: 6-9
6Pakuti pamene tinali cikhalire ofok a, pa nyengo yace Kristu anawafera osapembedza. 7Pakuti ndi cibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. 8Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife. 9Ndipo tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.

1 Timoteo 2: 1-6
1Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse; 2cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse. 3Pakuti ici ncokoma ndi colandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; 4amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi. 5Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu, 6amene anadzipereka yekha ciombolom'malo mwa onse; umboni m'nyengo zace;

Yakobo 4: 7-10
7Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. 8Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu. 9Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni. 10Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

2 Petro 3: 9
9Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

Ahebri 11: 6
6koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.

Mateyu 11: 27-30
27Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha; ndi palibe wina adziwa Atate, koma M wana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira. 28Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. 29Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30Pakuti 1 gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Funso #1

Masalmo 46:10
10Khalani cete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu: Ndidzabuka mwa amitundu, Ndidzabuka pa dziko lapansi.

Masalmo 145: 18-19
18Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, Onse akuitanira kwa Iye m'coonadi.
19Adzacita cokhumba iwo akumuopa; Nadzamva kupfuula kwao, nadzawapulumutsa.

Yesaya 55: 3
3Cherani Lhutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu cipangano cosatha, ndico zifundo zoona za Davide.

Ahebri 10:22
22tiyandikire ndi mtima woona, m'cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Funso #2

Yohane 14: 6-7
6Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
7Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye.

1 Yohane 1: 5
5Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima.

Aroma 3: 20-24
20cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi Debito za lamulo; pakuti ucimo udziwika ndi lamulo.
21Koma tsopano cilungamo ca Mulungu caoneka copanda lamulo, cilamulo ndi aneneri acitira ici umboni; 22ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana; 23pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;24ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;

Ezekieli 18:32
32Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; cifukwa cace bwererani, nimukhale ndi moyo.

Aroma 3:23
23pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

Macitidwe 4:12
12Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwanalo.

Have You Received God's Gift of Salvation?

Funso #3

Yohane 6:29
29Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.

Yohane 5:24
24Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo.

1 Yohane 5: 10-12
10Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; ye wosakhulupirira Mulungu ananuyesa iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana wace. 11Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace. 12Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

Funso #4

Yohane 3: 1-8
1Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda,2Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye, 3Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. 4Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa?
5Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. 6Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu. 7Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano. 8Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, komavsudziwa, kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.

Funso #5

Yohane 3:36
36Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.

Yohane 16:24
24Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.

Aroma 4: 7-8
7ndi kuti, Odala iwo amene akhululukidwa kusayeruzika kwao, Nakwiriridwa macimo ao, 8Wodala munthu amene Mulungu samwerengera ucimo.

Aroma 5: 1
1Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu;

2 Akorinto 5:17
17Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

Aefeso 1:13
13Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

Ahebri 13: 5
5Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Aefeso 1: 3-6
3Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu; 4monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi, 5Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana, a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace, 6kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.

2 Akorinto 5:21
21Ameneyo sanadziwa ucimo anamyesera ucimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale cilungamo ca Mulungu mwa iye.

Afilipi 3: 8-9
8Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale citayiko cifukwa ca mapambanidwe a cizindikiritso ca Kristu Yesu Ambuye wanga, cifukwa ca Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu, 9ndi kupezedwa mwa iye, wosati wakukhala naco cilungamo canga ca m'lamulo, koma cimene ca mwa cikhulupiriro ca Kristu, cilungamoco cocokera mwa Mulungu ndi cikhulupiriro;

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us