Project Hope     home >>stonecroft>> kodi yesu ndani? >> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #1
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Machitidwe 9:5
Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;

Marko 4:41
41Ndipo iwo anacita mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Mateyu 16:13-16
13Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kaisareya wa Filipi, anafunsa ophunzira ace, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani? 14Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri. 15Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani? 16Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.

Maliko 6:14-16
14Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace mphamvu izi zicitacita mwa Iye. 15Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya, Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo, 16Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo.

2 Mafumu 2:11
11Ndipo kunacidka, akali ciyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka gareta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kabvumvulu.

Exodo 3:14
14Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.

Yohane 5:18
18Cifukwa ca ici Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si cifukwa ca kuswa dzuwa la Sabata kokha, komatu amaehanso Mulungu Atate wace wa iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.

1. Yohane 21:25
25Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.

2. a. Mateyu 1:21
21Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao.

b. Mateyu 1:23
23Onani namwali adzaima, Nadzabala mwana wamwamuna,
Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe.

c. Mateyu 3:17
17ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.

d. Mateyu 12:8
8pakuti Mwana wa munthu ali mwini tsiku la Sabata.

e. Mateyu 16:16
16Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.

f. Mateyu 19:16
16Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, cabwino nciti ndicicite, kuti ndikhale nao mayo wosatha?

3. a. Marko 5:6-7
6Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye; 7ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Ndiri ndi ciani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.

b. Luka 5:5
5Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.

c. Yohane 1:35-36
35 Pa tsiku lotsatira Yohane analinso pamenepo pamodzi ndi awiri a ophunzira ake. 36 Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”

d. Yohane 1:49
49Natanayeli anayankha Iye, Rabi, 14 Inu ndinu Mwana wa Mulungu, 15 ndinu Mfumu ya Israyeli,

e. 1 Akolinto 1:6-7
6mongaumboni wa Kristu unakhazikika mwa inu; 7kotero kuti sicikusowani inu caufuru ciri conse; pakulindira inu bvumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu;

4. Mateyu 1:1-17
1BUKU la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ace; 3ndi Yuda anabala Farese ndi Zara mwa Tamare; ndi Farese anabala Ezronu; ndi Ezronu anabala Aramu; 4ndi Aramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala Salimoni;5ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabe; ndi Boazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jese; 6ndi Jese anabala Davide mfumuyo.
Ndipo Davide anabala Solomo mwa mkazi wa Uriya; 7ndi Solomo anabala Rehabiamu; ndi Rehabiamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa; 8ndi Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;9ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya; 10ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya; 11ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ace pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babulo.
12Ndipo pambuyo pace pa kutengedwako ku Babulo, Yekoniya anabala Salatieli; ndi Saiatieli anabala Zerubabele; 13ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro; 14ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi; 15ndi Eliyudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo; 16ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wace wa Mariya, amene Yesu, wochedwa Kristu, anabadwa mwa iye.
17Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babulo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babulo kufikira kwa Kristu mibadwo khumi ndi inai.

Yohane 2:1-11
1Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amace wa Yesu anali komweko. 2Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace anaitanidwa ku ukwatiwo. 3Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo,4Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.5Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri conse akanena kwa inu, citani.
6Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu. 7Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde. 8Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwamkulu wa phwando. Ndipo anapita nao. 9Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwa kumene anacokera (koma atumiki amene adatiinga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati, 10nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino. 11Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira iye.

Marko 1:9-11
9Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kucokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordano. 10Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: 11ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.

Yesaya 9:6
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

Akolose 1:15-20
15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse; 16pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye. 17Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye. 18Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale iye mwa zonse woyambayamba. 19Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire, 20mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.

15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo,
wobadwa woyamba wa cilengedwe conse; Akolose 1:15-20

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us