Project Hope     home >>stonecroft>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1 >> phunziro 2
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #2
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Mateyu 5:1-12
1Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ace; 2ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:
3Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.
5Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.
6Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.
7Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.
8Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.
9Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.
10Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
11Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.
12Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

Mateyu 5:13-16
13Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. 15Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali m'nyumbamo. 16Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mateyu 6:1-15
1Yang'anirani kuti musacite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.2Cifukwa cace pamene pali ponse upatsa mphatso zacifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amacita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 3Koma iwe popatsa mphatso zacifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe cimene licita dzanja lako lamanja; 4kotero kuti mphatso zako zacifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
5Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 6Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. 7Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao. 8Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye. 9Cifukwa cace pempherani inu comweci:
Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. 10Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano. 11Mutipatse ife lero cakudya cathu calero. 12Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. 13Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.
14Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. 15Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

Mateyu 6:24-34
24Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina.
Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma. 25Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala? 26Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
27Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?28Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota: 29koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa. 30Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? 31Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani? 32Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. 33Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. 34Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.

Mateyu 7:1-12
1Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. 2Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. 3Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? 4Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. 5Wonyenga iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.
6Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
7Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo cidzatsegulidwa kwa inu; 8pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo citsegulldwa. 9Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wace mkate, adzampatsa mwala?10Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? 11Comweco, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? 12Cifukwa cace zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu acitire inu, inunso muwacitire iwo zotero; pakuti ico ndico cilamulo ndi aneneri.

Mateyu 7:13-20
13Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa ico. 14Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.
15Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa. 16Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? 17Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa, 18Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma. 19Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto. 20Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.

Mateyu 7:21-27
21Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba. 22Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? 23Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika. 24Cifukwa cimeneci yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwacita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wocenjera, amene anamanga nyumba yace pathanthwe; 25ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; cifukwa inakhazikika pathanthwepo.
26Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawacita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yace pamcenga; 27ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwace kunali kwakukuru.

Yohane 8:56-59
5613 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona, nasangalala. 57Ayuda pamenepo anati kwa iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?
58Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo 14 Ine ndiripo. 59Pamenepo 15 anatola miyala kuti amponye iye; koma Yesu anabisala, naturuka m'Kacisi.

1. a. Yohane 13:19
19Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, cisadacitike, kuti pamene citacitika, mukakhulupire kuti ndine amene.

b. Yohane 8:12
12Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.

c. Yohane 10:9
9Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa.

d. Yohane 10:11
11Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa.

e. Yohane 10:36
36kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko lapansi, Ucita mwano; cifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?

f. Yohane 11:25
25Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;

g. Yohane 6:48
48 Ine ndine mkate wamoyo,

h. Yohane 14:6
6Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

3. Mateyu 5:21-26
21Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu: 22koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wace wopanda cifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wace, Wopanda pace iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akuru: koma amene adzati, Citsiru iwe: adzakhala wopalamula gehena wamoto.
23Cifukwa cace ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, 24usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nucoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako. 25Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende. 26Indetu ndinena ndi iwe, sudzaturukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumariza ndiko.

Mateyu 5:3-12
3Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.
5Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.
6Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.
7Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.
8Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.
9Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.
10Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
11Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.
12Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

Mateyu 5:13-16
13Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. 15Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali m'nyumbamo. 16Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mateyu 5:17-20
17Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa. 18Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.19Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.20Pakuti ndinena ndi inu, ngati cilungamo canu sicicuruka coposa ca alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Mateyu 5:27-30
27Munamva kuti kunanenedwa, Usacite cigololo; 28koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kucita naye cigololo mumtima mwace.
29Koma ngati diso lake lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'gehena. 30Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losamuka thupi lako lonse kugehena.

Mateyu 5:31-32
31Kunanenedwanso, Yense wakucotsa mkazi wace ampatse iye cilekaniro:32koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakucotsa mkazi wace, kosati cifukwa ca cigololo, amcititsa cigololo: ndipo amene adzakwata wocotsedwayo acita cigololo.

Mateyu 5:33-37
33Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako: 34koma Ine ndinena kwa inu, 6Musalumbire konse, kapena kuchula Kumwamba, cifukwa kuli cimpando ca Mulungu; 35 kapena kuchula dziko lapansi, cifukwa liri popondapo mapazi ace; kapena kuchula Yerusalemu, cifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikurukuru. 36 Kapena usalumbire ku mutu wako, cifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. 37 Kama manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo coonjezedwa pa izo cicokera kwa woipayo.

Mateyu 5:38-42
38Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:39koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako Lamanja, umtembenuzire linanso. 40Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso copfunda cako. 41Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri. 42Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

Mateyu 5:43-48
43Munamva kuti kunanenedwa, 14 Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: 44koma Ine ndinena kwa inu, 15 Kondanani nao adani anu, ndi 16 kupempherera iwo akuzunza inu;
45kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; cifukwa Iye amakwezera dzuwa lace pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.
46Cifukwa kuti 17 ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? kodi angakhale amisonkho sacita comweco? 47Ndipo ngati mulankhula abale anu okha okha, mucitanji coposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sacita comweco?48Cifukwa cace inu 18 mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mateyu 6:1-4
1Yang'anirani kuti musacite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.2Cifukwa cace pamene pali ponse upatsa mphatso zacifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amacita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 3Koma iwe popatsa mphatso zacifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe cimene licita dzanja lako lamanja; 4kotero kuti mphatso zako zacifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.

Mateyu 6:5-15
5Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 6Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. 7Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao. 8Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye. 9Cifukwa cace pempherani inu comweci: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. 10Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano. 11Mutipatse ife lero cakudya cathu calero. 12Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. 13Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.
14Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. 15Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

Mateyu 6:16-18
16Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 17Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: 18kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.

Mateyu 6:19-21
19Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: 20koma mudzikundikire nokha cuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; 21pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.

Mateyu 6:22-23
22Diso ndilo nyali ya thupi; cifukwa cace ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa. 23Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Cifukwa cace ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukuru ndithu!

Mateyu 6:24-34
24Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma. 25Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?
26Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? 27Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?28Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:
29koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa.
30Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? 31Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani? 32Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. 33Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. 34Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.

Mateyu 7:1-6
1Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. 2Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. 3Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? 4Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. 5Wonyenga iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.
6Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.

Mateyu 7:7-12
7Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo cidzatsegulidwa kwa inu; 8pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo citsegulldwa. 9Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wace mkate, adzampatsa mwala?10Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? 11Comweco, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? 12Cifukwa cace zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu acitire inu, inunso muwacitire iwo zotero; pakuti ico ndico cilamulo ndi aneneri.

Mateyu 7:13-14
13Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa ico. 14Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.

Mateyu 7:15-20
15Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa. 16Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? 17Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa, 18Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma. 19Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto. 20Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.

Mateyu 7:21-23
21Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba. 22Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? 23Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.

Mateyu 7:24-27
24Cifukwa cimeneci yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwacita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wocenjera, amene anamanga nyumba yace pathanthwe; 25ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; cifukwa inakhazikika pathanthwepo.
26Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawacita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yace pamcenga; 27ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwace kunali kwakukuru.

Mateyu 7:28-29
28Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi ciphunzitso cace: 29pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembiao.

1 Akolinto 2:13-16
13Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu. 14Koma munthu wa cibadwidwe ca umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, cifukwa ziyesedwa mwauzimu. 15Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense. 16Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize iye? Koma ife tiri nao mtima wa Kristu.

4. Mateyu 13:1-58
1Tsiku lomwelo Yesu anaturuka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja. 2Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.3Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anaturuka kukafesa mbeu, 4Ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo. 5Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya, Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; 6ndipo popeza zinalibe mizu zinafota. 7Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo. 8Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu. 9Amene ali ndi makutu, amve.
10Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?
11Ndipo Iye anayankha nati, Cifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo. 12Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zocuruka; koma yense amene alibe, cingakhale comwe ali naco cidzacotsedwa kwa iye.13Cifukwa cace ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; cifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. 14Ndipo adzacitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati.
Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; Pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse;
15Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa, Ndipo m'makutu ao anamva mogontha, Ndipo maso ao anatsinzina;
Kuti asaone konse ndi maso, Asamve ndi makutu, Asazindikire ndi mtima wao, Asatembenuke, Ndipo ndisawaciritse iwo.
16Koma maso anu ali odala, cifukwa apenya; ndi makutu anu cifukwa amva.17Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanaziona; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva.
18Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja. 19Munthu ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.20Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera; 21ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo. 22Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda cipatso. 23Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
24Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwace;25koma m'mene anthu analinkugona, mdani wace anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nacokapo. 26Koma pamene mmera unakula, nubala cipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. 27Ndipo anyamata ace a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? nanga wacokera kuti namsongoleyo? 28Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wacicita ici. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi? 29Koma iye anati, lai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.
30Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
31Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pace; 32kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.
33Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
34Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo; 35kuti cikacitidwe conenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;
Ndidzaulula zinthu zobisika ciyambire kukhazikidwa kwace kwa dziko lapansi.
36Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.37Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa munthu;38ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo; 39ndipo mdani amene anamfesa uwu ndiye mdierekezi: ndi kututa ndico cimariziro ca nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo. 40Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, matero mudzakhala m'cimariziro ca nthawi ya pansi pano.41Mwana wa munthu adzatuma angelo ace, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kucotsa mu Ufumu wace zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akucita kusayeruzika, 42ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 43Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.
44Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
45Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: 46ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatari, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.
47Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi 1 kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse; 48limene podzala, analibvuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. 49Padzatero pa cimariziro ca nthawi ya pansi pano: angelo adzaturuka, 2 nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, 50nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
51Mwamvetsa zonsezi kodi? lwo anati kwa Iye, inde. 52Ndipo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace, mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene aturutsa m'cuma cace zinthu zakale ndi zatsopano.
53Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anacokera kumeneko.54Ndipo 3 pofika ku dziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitengakuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?554 Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? kodi dzina lace la amace si Mariya? ndi 5 abale ace si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? 56Ndipo alongo ace sali ndife onsewa? Ndipo iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?57Ndipo iwo anakhumudwa cifukwa ca Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, 6 Mneneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwace.58Ndipo Iye, cifukwa ca kusakhulupirira kwao, sanacita kumeneko zamphamvu zambiri.

5. Luka 8:11-15
11Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu, 12Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nacotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.13Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka. 14Ndipo zija zinagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi cuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu. 15Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

7. Marko 8:38
38Pakuti yense wakucita manyazi cifukwa ca Ine, ndi ca mau anga mu mbadwo uno wacigololo ndi wocimwa, Mwana wa munthu adzacitanso manyazi cifukwa ca iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ace oyera, mu ulemerero wa Atate wace.

Marko14:72
72Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi.

Luka 24:5-7
5ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?6Palibe kuno iye, komatu anauka; kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya, 7ndi kunena, kuti, Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ocimwa, ndi kupacikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lacitatu.

Yohane 5:25-29
25Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha; 27ndipo anampatsa iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.28Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ace, 29nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

Yohane 12:32-33
32Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha. 33Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.

Yohane 5:25-29
25Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha; 27ndipo anampatsa iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.28Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ace, 29nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

Yohane 11:17-44
17Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai. 18Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yace yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; 19koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.
20Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba. 21Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. 22Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. 23Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka. 24Marita ananena ndi iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomariza. 25Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; 26ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici? 27Ananena ndi iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi. 28Ndipo m'mene anati ici anacoka naitana Mariya mbale wace m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe. 29Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa iye.30(Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye) 31Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko. 32Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. 33Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini, 34nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone. 35Yesu analira. 36Cifukwa cace Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi! 37Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kucita kuti sakadafa ameneyunso?
38Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo. 39Yesu ananena, Cotsani mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai. 40Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu? 41Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.
42Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire kuti Inu munandituma Ine. 43Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula ndi mau akuru, Lazaro, turuka. 44Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.

Mateyu 24:1-3
1Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo. 2Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?

Mateyu 24:36-39
36Koma za tsiku ilo ndi nthawi yace sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. 37Ndipo 1 monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.38Pakuti monga m'masiku aja, cisanafike cigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'cingalawa, 39ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira kumene cigumula cinadza, cinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.

8. Yohane 17:5-8
5Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi. 6Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu. 7Azindikira tsopane kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine zicokera kwa Inu; 8cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.

Yohane 7:45-46
45Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga iye bwanji? 46Anyamatawo anayankha, 7 Nthawi yonse palibe munthu analankhula cotero.

9. a. Marko 1:10-11
10Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: 11ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.

b. Yohane 1:32
32Ndipo Yohane anacita umboni, nati, 8 Ndinaona Mzimu alikutsika kucokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye.

c. Machitidwe 11:4-9
4Koma Petro anayamba kuwafotokozera cilongosolere, nanena, 5Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine; 6cimeneco ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga. 7Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye. 8Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse. 9Koma mau anayankha nthawi yaciwiri oturuka m'mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba.

Machitidwe 10:3-6
3Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lacisanu ndi cinai la usana, nanena naye, Komeliyo. 4Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nciani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zacifundo zako zinakwera zikhala cikumbutso pamaso pa Mulungu.

Machitidwe 13:2-3
2Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
3Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.

Aheberi 1:1-2a
1KALE Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyana-siyana, 2koma pakutha pace pa masiku ano analankhula ndi ife ndi

Miyambo 8:34-35
34Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku,
Ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;
35Pakuti wondipeza ine apeza moyo;
Yehova adzamkomera mnma.

1 Atesolonika 2:13
13Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira.

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us