Project Hope     home >>stonecroft>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 2 >> phunziro 3
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #3
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Marko 1:16-28
16Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi. 17Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. 18Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye. 19Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, iwonso anali m'combo nakonza makoka ao.20Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedayo m'combomo pamodzi ndi anchito olembedwa, namtsata. 21Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa, 22Ndipo anazizwa ndi ciphunzitso cace; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi. 23Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anapfuula iye 24kuti, Tiri ndi ciani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. 25Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli cete, nuturuke mwa iye. 26Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kupfuula ndi mau akuru, unaturuka mwa iye. 27Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ici nciani? ciphunzitso catsopano! ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.28Ndipo mbiri yace inabuka pompaja ku dziko lonse la Galileya lozungulirapo.

Marko 1:29-39
29Ndipo pomwepo, poturuka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane, 30Ndipo mpongozi wace wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:31ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
32Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda. 33Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. 34Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.
35Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko. 36Ndipo Simoni ndi anzace anali naye anamtsata,37nampeza, nanena naye, Akufunani inu anthu onse. 38Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene. 39Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, naturutsa ziwanda.

Marko 3:13-19
13Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. 14Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, 15ndi kuti akhale nao ulamuliro wakuturutsa ziwanda.16Ndipo Simoni anamucha Petro; 17ndi Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace wa Yakobo, iwo anawacha Boanerge, ndiko kuti, Ana a bingu; 18ndi Andreya, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani, 19ndi Yudase Isikariote, ndiye amene anampereka Iye.

Marko 4:35-41
35Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina. 36Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye. 37Ndipo panauka namondwe wamkuru wa mphepo, ndi mafunde angabvira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala. 38Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife? 39Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipokunagwa bata lalikuru.40Ndipo ananena nao, Mucitiranji mantha? kufikira tsopano mulibe cikhulupiriro kodi? 41Ndipo iwo anacita mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Marko 6:30-44
30Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza ziri zonse adazicita, ndi zonse adaziphunzitsa, 31Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya. 32Ndipo anacokera m'ngalawa kunka ku malo acipululu padera. 33Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira. 34Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. 35Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ace, nanena, Malo ana nga cipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu; 36muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya. 37Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya? 38Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, lsanu, ndi nsomba ziwiri. 39Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulu magulu pamsipu. 40Ndipo anakhala pansi mabungwe mabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu.41Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'anakumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo. 42Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. 43Ndipo anatola makombo mitanga khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba. 44Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.

Marko 10:2-16
2Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace, namuyesa Iye. 3Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulirani ciani? 4Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata wakulekanira, ndi kumcotsa. 5Koma Yesu anati kwa iwo, Cifukwa ca kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili. 6Koma kuyambira pa ciyambi ca malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi.7Cifukwa cace mwamuna adzasiya atate wace ndi amai wace, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wace; 8ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. 9Cifukwa cace cimene Mulungu anacimanga pamodzi, asacilekanitse munthu. 10Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za cinthu ici. 11Ndipo Iye ananena nao, Munthu ali yense akacotsa mkazi wace, nakakwatira wina, acita cigololo kulakwira mkaziyo;12ndipo ngati mkazi akacotsa mwamuna wace, nakwatiwa ndi wina, acita cigololo iyeyu.
13Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula. 14Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.15Ndithu ndinena ndi inu, Munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse. 16Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ace pa ito.

Yohane 2:13-22
13Ndipo Paskha wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. 14Ndipo anapeza m'Kacisiiwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi. 15Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m'Kacisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome; 16nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Cotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda. 17Akuphunzira ace anakumbukila kuti kunalembedwa, Cangu ca pa nyumba yanu candidya ine. 18Cifukwa cace Ayuda anayankha nati kwa iye, Mutionetsera ife cizindikilo canji, pakuti mucita izi? 19Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani kacisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.20Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi cimodzi analimkumanga Kacisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu? 21Koma iye analikunena za kacisi wathupi lace. 22Cifukwa cace atauka kwa akufa, akuphunzira ace anakumbukira kuti ananena ici; ndipo anakhulupirira colemba, ndi mau amene Yesu ananena.

Marko 11:15-17
15Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda; 16ndipo sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa Kacisi. 17Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.

Luka 1:29, 34; 2:19, 51
29Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulankhula uku nkutani. 34Koma Mariya anati kwa mngelo, ici cidzacitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna?
19Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.
51Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amace anasunga zinthu izi zonse mumtima mwace.

Yohane 1:1-3, 14
1PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu. 2Awa anali paciyambi kwa Mulungu, 3Zonse: zinalengedwa ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kali konse kolengedwa,
14Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.

1. a. Luke 3:23
23Ndipo Yesuyo, pamene anayamba nchito yace, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,

b. 1 Yohane 4:9
9Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.

2. a. Yohane 5:17
17Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira nchito kufikira tsopano, lnenso ndigwira nchito.

3. a. Marko 1:21
21Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa,

b. Marko 1:32-34
32Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda. 33Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. 34Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.

c. Marko 1:35
35Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko.

d. Marko 1:38
38Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.

e.Marko 6:7-12
Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza Iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa; 8ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao; 9koma abvale nsapato; ndipo anati, Musabvale malaya awiri. 10Ndipo ananena nao, Kumene kuli konse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukacokako. 11Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakucoka kumeneko, sansani pfumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. 12Ndipo anaturuka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.

Yohane 21:25
25Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.

Zozizwitsa Zake

4. a. Luka 4:33-36
33Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala naco ciwanda conyansa; napfuula ndi mau olimba, kuti, 34Ha! tiri ndi ciani ndi Inu, Yesu wa ku N azarete? kodi munadza kutiononga ife? ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wace wa Mulungu. 35Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nuturuke mwa iye. Ndipo ciwandaco m'mene cinamgwetsa iye pakati, cinaturuka mwa iye cosampweteka konse. 36Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzace, nanena, Mau amenewa ali otani? cifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingoturuka.

b. Luka 5:4-10
4Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza. 5Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka. 6Ndipo pamene anacita ici, anazinga unyinji waukuru wansomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika; 7ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira. 8Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa. 9Pakuti cizizwo cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola; 10ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

c. Marko 1:40-42
40Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza. 41Ndipo Yesu anagwidwa cifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa. 42Ndipo pomwepo khate linamcoka, ndipo anakonzedwa.

d. Mateyu 15:1-9
1Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ocokera ku Yerusalemu, nati,2Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? pakuti sasamba manja pakudya. 3Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu cifukwa ca miyambo yanu? 4Pakuti Mulungu anati,
Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, Wakunenera atate wace ndi amace zoipa, afe ndithu.
5Koma inu munena, Amene ali yense anena kwa atate wace kapena kwa amace, Ico ukanathandizidwa naco, neoperekedwa kwa Mulungu; 6iyeyo sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu.7Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti, 8Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.
9Koma andilambira Ine kwacabe, Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

e. Luka 7:11-17
11Ndipo kunali, katapita kamphindi, iye ana pita kumudzi, dzina lace Nayini; ndipo ophunzira ace ndi mpingo waukuru wa anthu anapita nave. 12Ndipo pamene anayandikira ku cipata ca mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amace ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye. 13Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi cifundo cifukwa ca iye, nanena naye, Usalire.14Ndipo anayandikira, nakhudza cithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. 15Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amace. 16Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace. 17Ndipo mbiri yace imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira.

Luka 3:21-22
21Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo, 22ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Cholinga Chantchito

5. a. Yohane 6:38
38Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndicite cifuniro canga, koma cifuniro ca iye amene anandituma Ine.

b. Yohane 7:16-17
16Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine. 17Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.

c. Afilipi 2:13
13pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma mtima kwace, ndiye Mulungu,

6. Aroma 12:2
2Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.

Genesis 1:27-28
Mulungu ndipo adalenga munthu mu chifanizo chache; m'chifanizo cha Mulungu adalenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi anawalenga. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, "Mubalane muchuluke; mudzadze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa somba za m'nanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa za moyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi."

Genesis 2:15
Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo namuika iye m'munda wa Eden kuti
aulime nauyanganire.

Genesis 3:17
Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mawu a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuza iwe kuti Usadyeko; "nthaka ikhale yotembeleledwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako."

7.a 2 Atesalonika 3:10
10Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ici, Ngati munthu safuna kugwira nchito, asadyenso.

b. Aroma 12:11
11musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

8. Aefeso 6:5-8
5Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukila kanthu kena, monga kwa Kristu; 6si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima; 7akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai; 8podziwa kuti cinthu cokoma ciri conse yense acicita, adzambwezera comweci Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

9. a. 1 Akorinto 10:31
31Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

b. 1 Akorinto 16:14
14Zanu zonse zicitike m'cikondi.

c. Akolose 3:23
23ciri conse mukacicita, gwirani nchito mocokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

Yohane 13:34-35
34Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace. 351 Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.

Eksodo 31:15
Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma la chisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lopumula, lopatulika la Yehova; aliyense ogwira ntchito tsiku la Sabata, aphedwe ndithu.

Mateyu 5:17
17Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.

Marko 6:31
31Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

Mateyu 11:28-30
28Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. 29Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30Pakuti 1 gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

10. a. Yohane 6:29
29Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.

b. Yohane 3:16
16Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

1 Akolinto 3:13-15
13nchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, cifukwa kuti yabvumbuluka m'moto; ndipo mota wokha udzayesera nchito ya yense ikhala yotani. 14Ngati nchito ya munthu ali yense khala imene anaimangako, adzaandira mphotho. 15Ngati nchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zace; koma iye yekha adzapulumutsilwa; koma monga momwe mwa noto.

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us