Project Hope     home >>stonecroft>>mfundo za paziphuinzitso za m'baibulo>>buku lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 1
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #1
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Baibulo limati
Chani za Yesu?

Yesu ndi Ndani?

Sauli, munthu wachiyuda amene amamanga ndi kupha akristu oyambirira, anafunsa funso lofunikira. Ndifunso lofunikira limene tingafunse. Anafunsa, "Ndinu ndani, Ambuye?"

Analandira yankho pompopompo "
Ndine Yesu amene ukumulondalonda..."
(Machitidwe 9:5).

Munthu waukaliyu (amene anapamgitsa chipolowe mu chalitchi choyambirira ku Yerusalem) analandira uthenga woyenera, anakhala munthu wosandulika. Anali atatakasidwa ndi chikhulupiriro chabodza. Ankaganiza kuti anali kukondweretsa Mulungu pochita ntchito zake zakupha, koma iye amkalondalonda Iye.

Timachita zomwezo, pamene tikukhulupirira zinthu zimene zili zabodza. Timachita zinthu zimene zili zoyipa kwa ife eni—nkhakhalenso kwa anzathu. Njira yokhayo kuti tikhale ndi chidziwitso chenicheni ndi kuzindikira ndi kukhulupirira choonadi. Maphunziro a Baibulowa akumana ndi chosowa chanu cha choonadi. Akukankhirani ku chitsime cha zoonadi zonse, Mau a Mulungu. Mulungu akuti,

“Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka,
koma mau anga sadzachokaHeaven.”

—Mateyu 24:35

Mau a Mulungu ndi oona ndipo adzaima mpaka kalekale. Anthu ali ndi zidziwitso zolakwika za Yesu.

People have many incorrect and strange ideas about Jesus. Since our behavior is influenced and motivated by what we believe, it is important that we have accurate information about who Jesus is, who God is and who we are. When you have finished this study, you will know beyond a shadow of a doubt who Jesus really is.

Mumakhulupirira kuti Yesu ndi ndani? Lero timamva maganizo osiyanasiyana. Ena amati ndiye amene anayambitsa chipembedzo....mtsogoleri wa nkulu wa chikristu...mphunzitsi wa nkulu wa chikhalidwe...munthu woyamba kuzunzidwa mwankhanza mum'bado wake.

Titha kudziwa zoona pokhapoka tikakhulupirira uthenga wochokera ku chitsime cha choonadi. Pali choonadi chimodzi—Mulungu. Watipatsa ife Buku, limene limatiuza m'mene tingamudziwire Iye komanso m'mene tingakhalire moyo womusangalatsa Iye ndi ife.

Yesu sali ngati m'modzi wa atsogoleri a chipembedzo pa dziko la pansi. Sali ngati munthu wankulu wa m'Baibulo ngati Abraham, Mose, kapena Davide. Nthawi zonse tikamalemba tsiku kapena chaka, timazindikira kuti zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo Yesu Khristu anabwera ndi kugawa mbiri m'magawo awiri:

Tsopano, tiwone zimene chipangano chatsopano chimanena za Yesu.

Kumayambiriro kwa utumiki wa Yesu, ngakhale ophunzira ake anafunsa chimene Yesu anali. Vundukulani pamene pali funso mu chipangano cha tsopano pa Marko 4:41.....Ophunzira ake adazindikira kuti sanali munthu wamba. ngakhale m'masiku amenewo, anthu anali ndi zidziwitso zachilendo za chimene Yesu anali.

Werengani Mateyu 16:13-16.......Anthu amadziwa sanali munthu wamba. Amadziwa anali winawake wapadeladela. Ankawona ngati ndi Yohane M'batizi, amene anadulidwa mutu, wa uka kwa akufa. (Maliko 6:14-16). Ena amati ndi Eliya, m'neneri wa Chipangano cha Kale amene anatengedwa kunka kumwamba osafa (2 Mafumu 2:11). Poti a Yuda amayembekezera kuti Eliya adzabweranso, anakhulupirira kuti Yesu ndi Eliya amene wabweranso ku dziko lapansi. Ena ankaganiza kuti Yesu ndi Yeremiya—mneneri wina wa Chipangano cha Kale amene anaphedwa zaka zakale zoyambirira. Onsewo amalakwitsa.

Tsopano, tsatani mu buku lanu lamaphunziro pa tsamba 8 pamene tikuwerenga gawo lina tsopano kuti tili ndi chidziwitso cha chenicheni cha chimene Yesu ali , Chimene Mulungu ali, ndi chimene ife tili. Mukamaliza maphunzirowa, mudziwa chenicheni cha chimene Yesu ali

Baibulo limatiuza zinthu zambiri zodabwitsa za Yesu. Mwachitsanzo, Yesu analipo chikhalire nthawi isanayambe. Malo ambiri mu Baibulo amafotokoza Yesu analipo pachiyambi dziko lisanalengedwe.

Baibulo limati,

“Ndipo Iye ali woyamba wa sonse. . .”
—Akolose 1:17



Yesu analipo asanabadwe ngati munthu. Wakhala ali chikhalire ndipo adzakhala mpaka muyaya. Palibe mtsogoleri wa chipembedzo amwene ananena kuti adzakhala muyaya, koma Yesu ananena. Anati,

“ . . . Asanayambe kukhala Abraham ndipo 'Ine ndiripo'.”
—Yohane 8:58

Izi zitanthauza Yesu analipo. INE AMENE NDILI ndi dzina la Mulungu.

Pa Exodo 3:14, zaka zikwi ziwiri Yesu asanabadwe, Mulungu anadzionetsera Yekha kwa Mose ngati "INE AMENE NDILI" Muchiheberi dzinali litanthauza kukhala kwa chikhalire.

Yesu anaziyerekeza Yekha ndi Mulungu (Yohane 5:18)


Chiphunzitso cha Yesu Khristu chinali choonadi. Sanabweze kapena kusintha zimene ananena. sanakaike, kulota kapena kuyankhula mosatsimikizika. Kafukufuku wa moyo wake anasonyeza mwa Iye munali umulungu wonse. Analibe tchimo. Amakhululukira tchimo. Amalandira malambiro.

Zonsezi zikutisonyezera Iye anali Mulungu. Yesu ndi wapadeladela. Upadeladela wake ukuonetseredwa mwa kubadwa kwache kudzera mwa namwali, Moyo wake wopanda tchimo, ziphunzitso zache zamphamvu zimene zinatembenuza dziko. zosenzi zikungosonyeza moyo wake wangwiro.

Kuzindikira Choonadi

Baibulo buku lofunika kuposa buku linalililonse pa dziko lonse. Kuwerenga Baibulo ndi kulilingalira limabweretsa kusintha kwapamwamba pa moyo wanu wa uzimu. Pamene muwerenga, kumbukirani ndi uthenga wa Mulungu kwa inu ngati munthu.

Ganizani mozama ndi mwapemphero za maphunziro mukuphunzirawa.
zifunseni mafunso awa:

Baibulo pa gawo ili likuti chani?
Zindikirani choona cha Mulungu

Baibulo pa gawo ili likuti chani?
Mvetsetsani chimene Mulungu akunena.




Mulungu akundilankhula chani?
Chitengeni choonacho muchichite pa moyo wanu.

Mwapempero lingalilani m'mene Mulungu akufunira kuti Muyankhe

Muvera lamulo kapena kusintha m'mene mumaonera zinthu?


Gulu lilandirane pakuwerenga gulu la ziganizo zotsatilazi

Uthenga wa Bwino

Mabuku oyambirira a Chipangano cha Tsopano sanalembedwe kukhala a mbiri ya Yesu. analembedwa ndi anthu osiyanasiyana kwa magulu osiyanasiyana ndi zifukwa zosiyanasiyana. mabuku amenewa amatchedwa uthenga wabwino.

Awiri amabukuwa—Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi Uthenga Wabwino wa Yohane—unalembedwa ndi anthu awiri amene anayenda ndi Yesu kwa zaka zitatu. anali mu gulu la anthu khumi ndi awiri amene Yesu adawasankha ngati atumwi. Pa mu chipangano cha Tsopano pali mndandanda wa mau amene akupereka tanthauzo la mau amene simukuwadziwitsitsa. Onani tanthauzo la mtumwi. . . . .

Kuyambira pa ndi gawo losonyeza maphunziro. izi zimathandiza mukafuna kufufuza kuchoka mu Baibulo za phunziro limene mukufuna kuphunzira. Mateyu adalemba uthenga wa bwino wa Mateyu kutsimikizira a Yuda kuti iye ndiye Mesiya amene adakhala akumufunafuna.

Yohane adalemba uthenga wabwino wa Yohane kutsimikizira owerenga kuti Yesu adali Mwana wa Mulungu.

Uthenga wa bwino wa Mariko udalembedwa ndi mnyamata Maliko, amene adagwira ntchito ndi Paulo komanso Barnaba ndi Petulo. Marko adalemba kwa amitundu kuwauza za Yesu ndi zimene adachita.

Uthenga wa bwino wa Luka udalembedwa ndi dotolo wa chihelena amene anapanga kafukufuku ndi ku fusa anthu amene anali kumudziwa Yesu.

Chifukwa uthenga wabwino uluonse umalembedwa kwa anthu osiyanasiyana, onsewo amayimira mbali zosiyana za moyo wa Khristu.


Tsopano, tikaona zimene Baibulo limakamba za Yesu Christu kuti ndi ndani. Pali zambiri zimene zimakamba za Yesu mu Chipangano cha kale ndi Chipangano cha Tsopano. Tionako zochepa mu chipangano cha tsopano pompano. Tiyambe ndi funso loyamba mu buku lathu lophunzirira.

Sankhani wina awerenge funso loyamba, werengani za buku limene likuyenderana ndi Baibulo, funsani funso. Patsani gulu lanu nthawi yo lemba mayankho mu mau awo mu mabuku awo wophunzirira.

1. Yohane anati chani pomaliza pa uthenga wake wabwino? Yohane 21:25 . . .

(Use your Bible or Africa Bible Verse Handbook


Tikadziwana ndi anthu timafuna tidziwe mayina awo. Mu Baibulo, mayina amafotokoza za mbiri za munthu kusiyana ndi muchikhalidwe chathu. Amafotokoza za chimene munthuyo ali ndi zimene amachita. Mbuye wathu ndi wankulu palibe amene angatiuze zonse zimene tingafune kudziwa za Iye.

Perekani ma vesiwa kwa anthu osiyanasiyana kuti afufuze. Auzeni akhale okonzeka kuwerenga akafunsidwa.

Poti pali ma vesi ambiri mu funso lachiwiri, kodi mungakonde kuti ambiri mwa inu mufufuze vesi ndi kuwerenga ku gulu?

a. Mateyu 1:21

b. Mateyu 1:23

c. Mateyu 3:17

d. Mateyu 12:8

e. Mateyu 16:16

f. Mateyu 19:16

Vesi lililonse likawerengedwa, mutha kulemba dzina kapena mayina a Yesu mu buku lanu lophunzirira.

2. Ndi mayina ena ati amene Yesu amatchulidwa mu buku la Mateyu?

a. Mateyu 1:21 . . . . .


Chimene Iye amatchedwa? . . . . . (Yesu)

Yesu atanthauza “Mpulumutsi.” Mbali yomaliza ya vesi tangowerengayi ikutiuza chifukwa chimene Yesu anapatsidwa dzina limene limathandauza Mpulumutsi. Adzapulumutsa anthu ku dipo limene akanapereka chifukwa cha machimo awo.


b. Mateyu 1:23 . . . . .

Dzina limene Mulungu adampatsa Iye limatchedwa ndani? . . . . . (Immanuel)
Vesilo limatiuza za Chimene dzinalo limaimira. Kodi Immanuel atanthauzanji? . . . . . (Mulungu nafe.)


c. Mateyu 3:17 . . . . .

Mulungu adamutcha ndani? . . . . . (Mwana, Mwana wokondedwa)
Kutanthauza kuti iyeyo ndiye Mwana Yekhayo wa padeladela wa Mulungu

d. Mateyu 12:8 . . . . .


Awa ndi maina awiri amene Yesu anadzitcha Yekha. Mainayo ndi ati? . . . . .
(Mwana wa Munthu ndi Mbuye wa Sabata)

Yesu amaulura kuti iye ndi munthu komanso ndi Mulungu. Amadzicha Yekha Mawna wa Munthu ndi


e. Mateyu 16:16 . . . . .

Mwana wa Mulungu mu malembo ena mbaibulo. Petulo anati Yesu ndi ndani? . . . . . (Mesiya, Mwana wa Mulungu wa moyo)

Mu vesi 17, Yesu anati Mulungu wavumbulutsira dzina limeneli kwa Petulo. Mu malingaliro a Yuda, Mesiya amathanthauza mtsogoleri wodzodzedwa ndi Muliungu.

Mwana wa Mulungu wa moyo amathandauza Yesu anali ofana ndi Mulungu ndipo ndi wachikhalire ndi Mulungu.

f. Mateyu 19:16. . . . .

Amatchedwa Yani? . . . . . (Mphunzitsi) Mphunzitsi amavumbulutsa choonadi, ndipo Yesu anavumbulutsa choonadi.

Funso lotsatira likutipatsa maina ambiri a Yesu. Dzina linalililonse latsopano likubvumbulutsa chikhalidwe chimene chikufotokoza za Iye momveka bwino. Lembani mainawa mu buku lanu lophunzirira pamene tikupitirira kuphunzira.

Poti pali mavesi ambiri pa funso la chitatu, wina aliyense asankhe vesi limodzi kuti awerenge:

a. Marko 5:6-7

b. Luka 5:5

c. Yohane 1:35-36

d. John 1:49

e. 1 Akolinto 1:6-7

Kodi wina akonda kuti ayambe kutiwertengera funso lachitatu ndi kuona mu buku lathu limene limayenderana ndi Baibulo mu gawo "a."?

3. Kodi Yesu amatchedwa yani mu mabuku limene likuyenderana ndi Bailo?
a. Marko 5:6-7. . . . .

Yesu amatchedwa ndani? . . . . . (Yesu Mwana wa Mulungu wa M'wamba W'wamba)

Yesu ndi dzina lache la padziko lino. Ngati Mwana wa Mulungu wa M'wamba M'wamba , ndi woyenera kulambilidwa ndi ife. Simoni Petulo anamutcha ndani? . . . . . (Mbuye)


b. Luka 5:5. . . . .

What did Simon Peter call Him? .... (Master)

Yesu ndi amene akhristu amamutumikira. ngati wokhulupirira, ndife adzakazi ake..


c. Joyane 1:35-36 . . . . .

Yohane m'batizi anati Yesu ndi ndani? . . . . . (Mwana wa Nkhosa wa Mulungu)

Dzina ili limasonyeza Yesu kukhala nsembe ya ngwiro yotumizidwa kukaphedwa chifukwa cha matchimo a anthu onse kulikonse ali. Pa Aloma 6:23 mphoto ya uchimo ndi imfa. Nsembe ya nkhosa mu Chipangano cha Kale (Levitiko 14:12-13) ikuyimirira infa ya Yesu Khristu. Mulungu anati adzatumiza nsembe ya ngwiro kukafera m'malo a anthu ochimwa. Chifukwa chake Yesu amatchedwa Mwanawankhosa wa Mulungu


d. Yohane 1: 49. . . . .


Mwana wa Nkhosa Mulungu. Kodi ndi maina awiri ati amene Natanieli anamucha Yesu pa tsambali? . . . . . (Mwana wa Mulungu, Mfumu ya Israeli)


e. 1 Akolinto 1:6-7 . . . . .

Paulo anamutcha yani apa? . . . . . (Mbuye Yesu Khristu)

Awa ndi maina atatu amene amakonda kugwiritsidwa ntchito ngati dzina limodzi. Tikamutcha mbuye, tikutanthauza tikugongera ku utsogoleri ndi ulamuliro wake wa u Mbuye.

Pali mayina ambiri okamba za Yesu amene tikanatha kuona kuti kodi Yesu ndi ndani?

Ophunzira amamucha Mbuye, Mphunzitsi. Anapereka moyo wawo ku ulamuliro wake. Mutha kufunsa, "Kodi Baibulo ndi buku lokhalo limene limatidziwitsa za Yesu."

Ayi, pali mabuku ena akale ambiri amene amatiuza za chimene Yesu anali. Si Baibulo lokha limene lingati phunzitse za Yesu—ngakhale kuti Baibulo ndi buku lokhalo limene limafotokoza za choonadi cha Yesu. Pali olemba ambiri amene analemba za Yesu ndi zimene amachita zo sintha moyo wa anthu mu nyengo Yake. nagati miukufuna kuwerenga phunzirori, muwerenge buku lotchedwa Evidence That Demands a Verdict lolembedwa ndi Josh McDowell.

Mukaona kuti mau obvuta kufotokoza kapena kunena mu Buku lano lotsogolera, musade nazo nkhawa pa za katchulidwe ka mauwo. Pitilizani.

Titha kuphunzira kuti Yesu ndi ndani pogwiritsa ntchito mabuku a chiyuda kapena achikunja. Ambiri olemba zambiri amamutcha Yesu ngati choonadi cha mbiri. Pali mabuku atatu ambiri: Makalata a Pliny (PLEHN-ee), amene anali govanala wa ku Asia; mabuku a Tacitus (TAS-ih-tuhs), amene anali katsiri wotsogola wa malamulo ndi Lives of the Caesars wolemba Suetonius (swee-TOH-nee-uhs), amene anali wophunzira ndi wolemba za mbiri ya munthu. Adziwa za mbiri a ku Romawa analemba za Yesu ndi za ophunzira ake.

Josephus (Joh-SEE-fus), Wodziwa za mbiri wa chi Yuda amene anabadwa mu chaka cha A.D. 37 amene anali wosakhulupirira , analemba zoona za kupachikidwa kwa Yesu. Ngakhale kuti Josephus samakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya, analemba izi zokhudzana ndi Yesu:

“Tsopano, panali munthu uyu wa nzeru , ngati nkoyenera kumutcha munthu, poti anali wochita ntchito za bwino, mpunzitsi wa anthu wa choonadi. Anakopa Ayuda ngakhale a Mitundu. Anali Khristu, ndipo pamene Pilato pa kukhumba kwa anthu akuluakulu mwa ife, analamula apachikidwe pa mtanda, iwo anankonda Iye poyamba sanantaye; poti anaonekeranso kwa iwo wamoyo pa tsiku la chitatu, monga momwe aneneri a uzimu analoserandi zikwi khumi za zinthu zodabwitsa zokhudza Iye. Ndipo mtundu wa Akhristu wotchedwa chifukwa cha Iye ukanalipo osatha mpaka lero.”

—Antiquities

Mu buku lache lotchedwa Evidence That Demands a Verdict, Josh McDowell akuti wosakhulupirira amene wafufuza za Yesu atha kudziwa mosakayika kuti Chipangano Cha Tsopano chitha kudalilika pa zokamba zake za Yesu. Wofufuza mwa chilungamo zanganyozere kapena kulimbikitsa zimene ena amanena kuti nkhani ya Yesu ndi nthano kapena zikhulupiriro chabe. Josh McDowell anati kufotokoza mwachindunji za Yesu sikungasokonewzedwe ."

Ndi maumboni ambiri zopezekeratu, tikuyenera kukhala ndi chitsimikizo chachikulu cha zimene Baibulo limanena za moyo wa Yesu.

Baibulo lonse limafotokoza za Yesu Christu Ma buku 39 oyambirira a Chipangano Cha Kale, amapereka mauneneri ambiri okhudzana ndi Iye. Ma buku ena onse 27 a Chipangano cha Tsopano, amafotokoza za mbiri ya moyo Wake pa dziko lapansi ngakhalenso moyo wake atauka kwa akufa. Mabuku anayi a Uthenga Wabwino —Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane—amapanga pafupifupi theka la Chipangano cha Tsopano. Ali ndi zambiri zofotokoza za Yesu.

Maumboni ena a mphamvu okhudza choonadi cha Baibulo amaonetseredwa kudzera mu mauneneri a Chipangano cha kale kukwaniritsidwa mu Chipangano Cha Tsopano. Chipangano cha Kale chili ndi mazana amauneneri okhudza kubwera kwa Mesiya, Yesu Khristu.

Tsopano tiyamba kuwerenga mulandirana mu ma buku athu ophunzirira. Ndiwerenga uneneri ndi kufaniziridwa kwake mu Chipangano Cha Kale. Ndipo mutha kumalandirana powerenga kukwaniritsidwa kwake mu chipangano cha tsopano.

Ma uneneri ochepa okhudza Mesiya

Uneneri

Kukwaniritsidwa

Adzabadwa mwa namwali. Kubadwa mwa namwali Yesu

Yesaya 7:14 (742B.C.)
Chifukwa chache Ambuye mwini yekha
adzakupatsani chizindikiro, taonani namwali
adzaima, nadzabala mwana wa mwamuna,
nadzamucha dzina lache Imanueli. (NASB)


Mateyu 1:22-23
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti, Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wa mwamuna dzina lace, Emanueli;
(ndilosandulika, “Mulungu nafe”).

Malo ake obadwira

Kubadwa kwa Yesu mu Betelehem.

Micah 5:2 (710B.C.)
Ambuye akuti, “Betelehemu Efrata, ndiwe
wa ngono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzatuluka wowereza mu Israyeli;
matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.

Mateyu 2:1a
Yesu adabadwa mu mzinda
wa Betelehemu wa Yudea mu nthawi imene Herodi adali mfumu.
Adzakanidwa ndi anthu Ache.

Yesu adakanidwa.

Isaiah 53:3 (712B.C.)
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wa zisoni, ndiwodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu ombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamulemekeza.

Yohane 1:11
Anadza kwa zache za Iye yekha, koma dziko silidamuzindikira Iye.
Adzaperekedwa ndi bwenzi Yesu adaperekedwa ndi m'modzi mwa ophunzira.
Salimo 41:9 (1062B.C.)
Ngakhale bwenzi langa leni leni, amene
ndamkhulupirira, ndiye amene anadyako mkate wanga, adandikwezera chidendene chache.
Marko 14:10
Ndipo Yudase Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka napita kwa ansembe akulu, kuti akampereke Iye kwa iwo.
Adzauka kwa akufa. Yesu anauka patatha masiku atatu m'manda.
Salimo 16:10 (1040 B.C.)
…akuti simudzasiya moyo wanga kumanda;
simudzalora okondedwa wanu avunde.


Mateyu 28:5-6
Koma ngelo anayankha nati kwa akaziwo,
"Musaope inu; pakuti ndidziwa inu muli kufuna Yesu, amene anapachikidwa. Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena .idzani muno mudzaone malo omwe anagonamo Ambuye.”


Ma ulosi onse anakwaniritsidwa mwa Christu, ngakhale anali opyoza umunthu wa Yesu.
Onani funso 4.


4. Ziganizo zili mmusimu zikukamba za mbiri za Yesu. Onani pa mafunso oti
muyankhe, ndi zofananiza malemba a chiganizo ndi mau oyenerera mbaibulo:

a. Makolo Ake .......................b. Ubatizo Wake .....................c. Wake choyamba chake



Glance over Mateyu 1:1-17. . . . . (a Makolo Ake)

Ngati wina ali ndi funso pa za mbado wa Yesu, zitha kuthandiza mutafotokoza izi:

“Mateyu 1:16: Chifukwa choti Maria anatenga pakati akanali namwali, Mateyu akunena
za Yosefe ngati mwamuna wa Maria, koma osati bambo a Yesu. Mbado wolembedwa
ndi Mateyu akufotokoza (mbando wobvomerezeka) kudzera mwa Yosefe. Mbado wa
Maria unalembedwa pa Luka 3:23-38.Maria ndi Yosefe anali mu mbado wa Davide.

Mateyu akufotokoza za mbado kuyambira kwa Abraham, Pamene Luka akuyambira kwa
Adam.. Mateyu akulembera kwa Ayuda, nde Yesu akuonetsedwa ngati ochokera kwa
Tate wao Abraham. Luka akulembera kwa Amitundu, nde akufotokoza za Yesu ngati
Mpulumutsi wa anthu onse.”

Glance over Yohane 2:1-11. . . . . Read verse 11 (c Wake choyamba chake)



Read Marko 1:9-11 . . . . .(b Ubatizo Wake)

Chipangano cha tsopano chanu chimakuwuzani za moyo wa Yesu ndi m'mene mungakhalire m'moyo wa Chikhristu.

When we need to read parts of the Old Testament refer to the Africa Bible Verse Handbook if you do not have a Bible.

Mbuye Yesu Christu ndi Mulungu nafe. Titha kuona kuti ndi Mulungu. Titha kuona kuti ndi
Mulungu tikawerenga ulosi wa kubadwa kwache ku Yesaya 9:6 . . . . . Onani Yesu
akutchedwa Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wa mphamvu, Atate wosatha, Kalonga wa
Mtendere.

Ndimayina ati amene ali mainanso a Mulungu? . . . . .

(Mulungu wa mphamvu ndi Atate Wosatha)

Baibulo limatiuza za mbiri za Yesu ndipo kufotokozera kwina kwa mphamvu kuli mu
Chipangano cha Tsopano pa Akolose 1:15-20. Onani zonse zimene zanenedwa za Yesu monga pa mavesi awa.. . . . .

Fundo ya yikulu tikuipeza pa vesi 15.


“Khristu ndi fanizo la Mulungu wosaonekayo..."
—Akolose 1:15

Tangolingalirani mphamvu ya fundoyi!

Sabata la mawa tidzaphunzira phunziro 2. Tidzaphunzira zimene Yesus ananena za Iye ndi
zimene anaphunzitsa. Mudzawerenga chiphunzitso cha Yesu pamene muwerenga Baibulo pa lanu pa tsamba 15. Musanabwere sabata ya mawa, yankhani funso mu Buku lanu
Lophunzirira.

Muli ndi funso?

Sangalalani ndi phunziro la sabata ya mawa. Tiyeni tiyamike Mulungu chifukwa cha danga
lophunzira mau Ake.

Pemphero Lotseka

Zikomo Ambuye Mulungu. Taphunzira za mbiri za Yesu mu phunziro ili. Tiphunzitseni za mbiri pamene tikupitiliza maphunziro awa. Tithanndizeni kupeza nthawi yowerenga phunziro ya sabata ya mawa. Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Buku Lothandiza

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us