Project Hope     home >>buku lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 5 >>phunziro 6
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #6
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Ndidzamuona Yesu?

Cholinga cha phunziro

• Kuzindikira kufunika kwa kuuka kwa Yesu Khristu ndi kumulandira m'moyo
mwathu.
•Kuzindikira Mkristu sangakhale m'moyo wa umulungu mwa mphamvu kapena
zinthu zake.
• Mwachidule onetserani zidzachitike ku tsogolo.
•Onetserani kufunika kogawana uthenga wabwinondi anzathu.

Pemphero

Wokondedwa Atate ku mwamba, Zikomo potiphunzitsa zambiri za chimene Yesu ali.
Tiphunzitseni tidziwe za mbiri kuchokera mu Buku Lanu pamene tikuphunzira phunzirori.
Tikufuna tidziwe ngati tidzamuonadi Yesu. Mu dzina lache, ame.

Fundo zotsogolera

Mudadabwapo, ndidzamuona Yesu? Zimenezo azyankhidwa mu kuwerenga kwathu kwa mau.

Munthu m'modzi awerenge mayankho onse ku maphunziro athu a Baibulo a sabata
ndi sabata. Kenaka, iwo ali ndi mayankho osiyana atha kunena.


Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:

(Use your Bible or Africa Bible Verse Handbook)

Werengani gawo la baibulo pansipa ndipo mulembe fundo ya tanthauzo logwira
ntima limene malimva pa kuwerengedwa kulikonse.

Yohane 1:14-18

Yohane 14:1-11

1 Yohane 5:10-12

Mateyu 16:24-27

Afilipi 2:5-11

1 Atesolonika 4:15-18

Yohane 5:24-29

Taphunzira mayankho a mafunso ambiri mu phunziro ili. Funso loyamba ndi kubwereza
zonwe taphunzira.

1 a. Yesu ndi ndani kwa inu? . . . . .


Ena ayankha ponena ndi Mpulunutsi wawo, ena ati ndi Mulungu, ena adzamutcha
ndi maina Ache.Gulu liyankha malingana ndi kufunika kwa Khristu m'moyo wawo ndi
zimene aphunzira pa maphunzirowa.


b. Kodi Yesu anati lamulo lofunikira kwambiri ndi liti? Mateyu 22:36-40 . . . . . (Konda Mulungu ndi mtima wako onse.)

M'mau ochepa, Yesu watiuza m'mene tingakhalire moyo wa chikhristu.
kukonda Mulungu ndi mtima wathu onse, ndi kukonda wina aliyense. Pochita izi,
tikumvera zonse zimene malamulo onse a Mulungu.

c. Yesu anachita zinthu zambiri zofunika akanali pa dziko lapansi. Ntchito yofunikira
kwa mbiri ndi chifukwa chimene anabwerera. Chimnali chani? Marko 10:45 . . . . . (kupereka moyo wake chifukwa cha machimo athu kuti tiomboledwe)

Kusankha kuti amumvera Iye kapena ayi. Mulungu adadziwa anthu azasankha kuchimwa
osati ku mvera Iye. Pakudziwa ichi, Mulungu anapangiratu njira yoti munthu akhululukidwe
ndi kukhalanso pa chiyanjano ndi Iye.

2. Lembani mu magawo awa. sankhani ku mau awa:

mlowa malo fuko chosatheka kufa thupi
losachima kubadwa mwa namwali
makumi anayi Mulungu kuikidwa
m'manda kulipira kulamulira chikhululukiro
umuyaya chitatu mtanda mwana
wa nkhosa tchimo

Dipo (Mulungu) analilamula kuti lichitike pa pa anthu ochimwa inali (imfa). Nthawi
isanayambe, Mulungu anati osalakwa (olowa m'malo) kufa m'malo a munthu
ochimwa.Anthu amapereka sembe ya nyama yopanda banga—makamaka
(nkhosa)—akafuna Mulungu kuwakhululukira machimo awo. Mwazi wa nkhosa
umene anaupereka sunachots (tchimo). Inali chifanizo cha nsembe yoyera imene
Mulungu anayitumiza. Imaphimba tchimo lawo, kufikira Yesu kubwera pa dziko
(ndikudzafa) chifukwa cha machimo a dziko lapansi.

Koma kufa, Amayenera kukhala ndi thupi la munthu (thupi), chifukwa anali
Mulungu, ndipo kunali (kosatheka) kuti Mulungu afe. Chifukwa chache, anasankha
ndi kukonzekeretsa (fuko) limene anakonzekeretsa thupi la Iye. (anawapatula) iwo
ku (mafuko) a dziko lapansi ndikuwapatsa malamulo kuti atsate a kukhala mwa
(chiyero)

Nthawi itakwana, malingana ndi dongosolo Lache, anabwera ku Dziko ngati
Myuda, (vwobadwa mwa namwali) mwana. Anakhala m'moyo (wosachimwa)
(anayikidwa m'manda) koma pa tskiku (lachitatu) Anawuka kwa akufa,
kudzionetsera Yekha anali wa moyo. ataonedwa ndi anthu ambiri kwa masiku
makumi anayi, Anakwera ku mwamba.

Ngongol (idaperekedwa) younse. Mbali yathu ndi kulandira (chikhululukiro) cha
Mulungu ndi mphatso ya moyo (wosatha). Ichi chitanthauza tikulandira imfa ya
Yesu pa mtanda ngati dipo la matchimo athu. Timalola This means that we accept
Jesus Christ’s death on the cross as payment for our personal sin debt. Timalola
Mulungu (alamulire) miyoyo yathu.

Kodi chifukwa chani ndikofunika kuti wina aliyense adziwe zinthu izi? ndizofunika chifukwa chikhulupiriro chmapanga chikhalidwe. Chimene timakhulupirira chimapanga chimene timachita ndi m'mene timachitira. Chifukwa chake ndikofunika kukhala ndi kumvetsetsa kwa bwino za chimene Yesu ali.

Chikhulupiriro chimaumba Chikhalidwe.

Mochulukira tikudziwa ndi kukhulupirira za chikhalidwe chenicheni cha Mulungu, mochulukira tidzalingallira za Iye ndipo mochulukira tidzakhumba kukhala m'moyo wa chiyero, wangwiro ndi omvera.

Mau a Yesus ndi ntchito zache zinaonetsera kuti ndi Messiah. Kubwera kwake kunaloseredwa zaka zambiri, koma anthu sanakhulupirire.Anayenera kusankha kukhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu-Messia-kapena kukana kuti sanali chimene amanena kuti anali

Sabata yatha tinakambirana za m'mene tingayambire moyo wa Chikhristu poitana Yesu
Khristu kuti alowe m'moyo wathu ndikudzipereka kwa Iye.

Kodi alipo amene ali ndi funso pa za moyo wa tsopano mwa Christu?.....Kodi alipo wina
amene angatiuze za m'mene moyo wake wasinthira kuyambira atakhala Mkristu?

Ngati tili nawo ena mu gulu amene ali ndi mafunso okhudzana ndi chipulumutso,
apatseni kabuku koti
Mukhulupirira? ndipo werengani pamodzi ngati simunapange
izi mu phunziro 5.

Tsopano, titha kuyankha funso mu mutu wa phunziro lathu. Kodi Baibulo limati chani za
zoti tidzomuona kapena sitidzamuona Yeus? yankho lili mu funso lotsatira mu mabuku
athu ophunzirira.

3. Yesus akabwera msogolo, adzamuone ndani? Chibvumbulutso 1:7 . . . . . (Aliyense, Kuphatikizapo iwo amene akufuna kudzamuona Iye, kuphatikizapo iwo sakufuna kumuona Iye.)

Ngati wina angafunse kuti "iwo anamulasa" limathanthauza chain -
Yohane 19:33-34.

Ofufuza za Baibulo samagwirizana pa za nthawi yeni yeni imene Yesu adzabwera, poti
masiku ake mu baibulo sanalembedwe. Titha kukhala okonzeka podziwa kuti zidzachitika
mu nthawi yoikika ndi Mulungu.

Wina aliyense adzamuona. koma ena adzakhala ndi chidwi kumuona kusiyana ndi wena.
Tonse tidzagwada-ena mumupembedza ena momuopa.

4.Baibulo limati kudzakhala nthawi ya masautso ndi chizunzo pa dziko la pansi.
Werengani zimene zidzachitike pa dziko Yesu asanabwerenso, ndipo mulembe
zimene zakupatsani chidwi powerenga izi.

a. Mateyu 24:21-31

b. Marko 13:32-37

c. Luka 21:25-28, 34-36


5. Kodi chimachitika n'chiyani munthu akamwalira? Ahebri 9:27. . . . .(Chiweruzo.)

Chofunikira kwambiri kuti tichite tsopano, ndikuonetsetsa kuti tamulandira Yesu Khristu ngati Yekhayo amene angatipulumutse ku chilango cha Mulungu pa tchimo. Ngati talandira Khristu, chiweluzo chikudza ndi chokhacho cha zinthu zimene tinachita. Tione Baibulo limati chani za ichi.


6. a. 2 Akorinto 5:10 . . . . . (Tonse timalandira mphoto yotiyenera, malingana ndi m'mene tamutumikirira Iye.)

b. Machitidwe 17:30-31. . . . . (Khristu, amene anauka kwa akufa, adzaweruza dziko lonse ndi chilungamo.)

c. Chibvumbulutso 20:11-15 . . . . . (Ngati dzina la munthu silinalembedwa mu buku la moyo, adzaponyedwa mu nyanja ya moto.)

Anthu akamakamba za kupulumutsidwa, amakamba za kupulumutsidwa ku chilango chosatha mu nyanja ya moto.

Tikamawerenga za chimene Mulungu amanena za chiwerezo chache cha chilungamo, timazindikira kuti kulandira Yesu kumatipulumutsa ife kuchilango chotiyenera. Tikuyenera kukhala ofuna kudzipereka mwathunthu kwa Iye. Mitima yathu ikhale yodzala ndi matamando kwa Iye pa chipulumutso chake chachikulu!

Kodi ndi ndani amene Mulungu akufuna kupulumutsa? 1 Timoteyo 2:3-4. . . . . (Aliyense)

Mulungu safuna alo munthu m'modzi apite ku gahena. Iye anapangira gahena
kukhala ya satana ndi amithenga ake.—osati anthun (Mateyu 25:41). Anthu ali
omasuka kusankha Mulungu kapena satana.

Werengani Afilipi 2:10-11. . . . . Izi zikutiuza anthu adzagwada pa maundo awo ndi kubvomereza, "Yesu Khristu ndi Mbuye." Anthu ambiri sanena kuti Yesu ndi Mbuye panopa, koma ikudza nthawi yomwe aliyense adzaona chimene Iye ali ndi kubvomereza. Koma idzakhala nthawi itatha.

Tsiku likubwera limene Yesu adzabweranso pa dziko lapansi! Zonse zimene anthu
anakundika pa dziko lino zidzaonongedwa. Tsekulani pa 1 Yohane 2:15-17 . . . . . Izi zikutiuza kuti onse amene ayika chikhulupiriro chao pa zinthu za padziko lino adzazitaya, poti za padziko zidzapita. Tidzaweluzidwa ndi zimene talora Yesu kuchita mwa ife ndi kudzera mwa ife.

Tikalandira Yesu timasinthidwa 2 Akolinto 5:17. . . . . Tikakhala ndi moyo wake mwa ife, timasanthulika. Sitikhalanso akapolo a tchimo. Yesu amatsimikizira kuti upulumuka kapena ayi, kaya tipatsidwa mphoto kapena ayi.

Mwa ife wapeza kale chipambano. Tili nayo mphamvu yakukaniza satana. Mzimu wa
Mulungu mwa ife umafuna tidzimvera Mulungu. Pamene tasankha kuchita zomwe Mzimu
wa Mulungu akufuna tichite, timakhala m'moyo winanawina. Pali nthawi zina zimene
timapanga zisankho zolakwika ndi kuchita zomwe tikufuna. M'mawu ena, timachimwa.
Tikuyenera kukumbukira zomwe tauzidwa kuchita, 1 Yohane 1:8-10 . . . . .

Tikuyenera kubvomereza ndikubwenzeretsa ubale wathu ndi Mulungu. Tikadalira mwa Yesu, tichite chani? 1 Yohane 4:7-11. . . . . (lolani chikondi chilamulire zimene timachita ndi kunena)

Tikalapa, timabwerera kusiya za moyo wakale wosakhala ndi Mulungu ndi kukhala moyo wosangalatsa Mulungu. Timasankha kumvera Iye. Chimenecho ndi chifukwa chimodzi chimene timawerengera mawu a Mulungu-kuti tidziwe zimene Iye amafuna ife kuti tichite.

Khalani mukudziwa za Umuyaya!

7 a.Kozi zimene maphunzira zikupindura chani pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku?
2 Akorinto 7:1 . . . . . (Mayankho adzakhala osiyana ndipo adzakhalanso ndi fundo zochokera apa)

b. Kodi maonedwe anu pa zakukhala ndi zinthu ndi zimene mukulingalira mutatenga ndi kukhala nazo asintha motani? Mateyu 6:19-21 . . . . . (Ngati mukufuna zamnbiri, werenganinso 1 Yohane 2:16-17.)

c.Kodi zoti Mzimu Woyera akukhala mwa okhulupirira zimathawathandizira bwanji m'maonedwe awo pa za ziphinjo ndi zokhumudwitsa? Yakobo 1:2-4 .. . . . (Aziziona amwayi akamakumana ndi mayesero.)

d. Kodi chidziwitso cha dongosolo la Mulungu chikuyenera kuchita chani pa maonedwe a okhulupirira pa za kugawa uthenga wabwino kwa wena. 2 Timothy 4:1-5. . . . . (Okhulupirira akuyenera alalikire Uthenga Wabwino modekha ndi mokakamira posatengera kuti ena aulandira bwanji)

e. Kodi 1 Akorinto 15:58, amalimbikitsa bwanji okhulupirira kuti akhale wamachawi mu ntchito ya Mulungu? . . . . . (Zonse zimene wokhulupirirra amachita mu utumiki wa Ambuye ndi zantengo wapatali)


Ngati Akhristu, tikuyenera kugwiritsa ntchito nthawi yathu pa dziko lino kuwuza
wena za chipulumutso!

8. Maphunziro a Mau a Mulungu amasintha miyoyo. Maphunziro awa akusinthani
bwanji myo wanu? ..........(Limbikitsani onse kuti afotokoze mayankho awo)

Mnene funsoli layankhidwira lifotokoza za kumvetsetsa kwawo kwa chipulumutso
ndikuwunikira pamene pakufunika kufotokozera. Gawo linali lithandiza.

Ndife ana a Mulungu tikamulora Yesu kuti atikhululukire machimo athu ndikutipatsa moyo
wosatha chifukwa cha nsembe Yake kwa ife pa mtanda. Yesu ndi Mpulumutsi wathu,
Mulungu ndi Tate wathu ndipo Mzimu woyera amakhala mwa ife kutiunikira nthawi ndi
nthawi.

Ambuye akukonza malo a okhulupirira kuti akakhale mukupezeka kwake muyaya.
Sikudzakhala tchimo kapena imfa kumeneko, ndipo Baibulo limati mukupezeka kwake
muli zokoma za muyaya (Masalimo 16:11)!

Kuzindikira malonjezano a Mulungu zimatithandizira kupirira ku mayeselo, zokhoma, ndi
zofoketsa zimene zimabwera m'moyo uno ndi kutilimbikitsa kuti tikhale tikulimba mtima
mu nthawi yochepa tilikhale pa dziko lapansili. Okhulupirira akuyembekezera kudzakhala
muyaya m'malo abwino amene Mulungu anawakonzera.

Tsopano titha kuyankha funso la phunziro lathu, "Ndidzamuona Yesu?".......(Alileyense adzamuona Yesu ndipo adzabvomereza ali Ambuye)

Tisanatseke ndi pemphero, alipo amene akufuna kutiuza za pemphero limene analemba pa funso lachisanu ndi chinayi?

9. Lembani pemphero kufotokozera mathokozo anu kwa Mulungu potumiza Mwana
Wake, Yesu Khristu. Pazokambirana, mudzakhala ndi kusankha kogawa pemphero
lanu. Lembani pempher lanu apa.

Pemphero Lotsekera

Tate wathu wakumwamba, zikomo chifukwa chobwera pa dziko kudzatifera, zikomo chifukwa chobwera pa dziko mkudzadzitengera chilango machimo athu. Zikomo polola kukhala m'moyo wathu. Zikomo chifukwa cha lonjezo simudzatisiya tokha! Tithandizeni kupereka miyoyo yathu kuti uilamulire. Malizani zimene mayamba m'moyo wa wina aliyense. Tapemphera mu dzina la Yesu, Ameni.

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Buku Lothandiza

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us