Project Hope     home >>stonecroft>> yesu ndani? >>phunziro 2 >>phunziro 3
Stonecroft - YESU NDI NDANI?- Phunziro #3
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Yesu Anachita Chani?

Pemphero

Wokondedwa Mulungu, Baibulo limatiuza Yesu ndi Mwana Wanu. Limatiuza ali ndi
chikhalidwe ndi chilengedwe cha Inu. Tiphunzitseni tidziwe choonadi cha Yesu pamene
tikuphunzira. Tapemphera mu dzina la Yesu, ame..


Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:

Marko 1:16-28,

Marko 1:29-39,

Marko 3:13-19,

Marko 4:35-41,

Marko 6:30-44,

Marko 10:2-16,

Yohane 2:13-22,

Yesu amagwira ntchito

1 a. Kodi Yesu anali ndi zaka zingati pamene amayamba utumiki wake?
Luke 3:23

b. Anatumiza Yeus kudziko ndani? 1 Yohane 4:9

2 a. Chimene Yesu amanena kuti atate wake amachita ndi chani?
Yohane 5:17

b. Chifukwa cha ichi, ndichani chimene Yesu ananena kuti wayenera?. . . . .

3. Nenani mau ochepa zimene mwa izi zili mBaibulo zimavumbulutsa za zimene
Yesu anachita

a. Marko 1:21

b. Marko 1:32-34

c. Marko 1:35

d. Marko 1:38

e. Marko 6:7-12

 

Zozwizwitsa Zache

4. Zozwizwitsa Yesu anachita zinabvumbulutsa mphamvu Zache zimene
zinapatsidwa ndi ulamuliro wa Mulungu pa zinthu zonse:

chikhalidwe,................ imfa, .................ziwanda, ................zozwizwitsa, ...................matenda

Werengani ma mirakuli awa ndipo muzilinganize ndi mau oyenerera mu baibulo.

Mamirakuli mphamvu pa

a. Luka 4:33-36 . . . . . . . . . . . . . . . . . . .

b. Luka 5:4-10 . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .

c. Marko 1:40-42 . . . . . . . . . . . . . . . . . .

d. Mateyu 15:1-9 . . . . . . . . . . . . . . . . .

e. Luka 7:11-17 . . . . . . . . . . . . . . . . . . .

“Mphamvu yache ndiyotani mwa ife okhulupirira. . . .”

—Aefeso 1:19

 

Cholinga cha ntchito

5 a. Ntchito ya Yesu inali chani?
Yohane 6:38

b. Tingadziwe bwanji kuti zimene Yesu amanena zimachoka kwa Mulungu?
Yohane 7:16-17

c. Tikangodziwa cholinga cha Mulungu, Amatithanndiza bwanji?
Afilipi 2:13


6. Mulungu amapangitsa okhulupirira kukhala moyo wa bwino mu dziko
loyipa. Aroma 12:2



7. Chipangano cha Kale chimatsindika kuti Mulungu amaitana anthu kuti akagwire
ntchito. Kodi baibulo limati chani pa za ntchito?

a. 2 Atesalonika 3:10

b. Aroma 12:11




8. Lembani ma vesi awa, kulowetsa m'malo “olembedwa ntchito” kwa “akapolo” ndi
“olemba ntchito” kwa “mbuye.” Aefeso 6:5-8 . . . . .

9. Kodi ma vesi awa amatiuza chani m'mene tikuyenera kugwirira ntchito?

a. 1 Akorinto 10:31

b. 1 Akorinto 16:14

c. Akolose 3:23

Ngati tipanga zonse ku ulemerero wa Mulungu, ntchito zathu zonse
ziyeretsedwa —
kutanthauza zimapaturidwa ku kugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu


10 a. Mulungu watiuza zimene Iye akufuna tichite pa Yohane 6:29. Ndi chani? . . . . .

b. Mulungu anatumiza Ndani? Yohane 3:16

11. Yamikani ambuye pa ntchito imene machita. Muuzeni m'mene mukumvera za
ntchitoyo. Lembani pemphero apa.

Pemphero Lotsekera

Atate athu akumwamba, zikomo chifukwa cha ntchito mwatipatsa kuti ife tichite ndi
kutipatsa chitsanzo. Tikufuna musangalale nafe monga umo munasangalalira ndi Yesu.
tikufuna zonse tizichita zibweretse ulemerero ku dzina lanu. Tapemphera mu dzina la
mphamvu la Yesu Khristu, ame.

 
 

 

YESU NDI NDANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us