Project Hope     home >>stonecroft>> yesu ndani? >>phunziro 3 >>phunziro 4
Stonecroft - YESU NDI NDANI?- Phunziro #4
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Chifukwa chani Yesu anabwera?

Pemphero

Wokondedwa Atate a Kumwamba, zikomo pa zonse matiphunzitsa za Mwana Wanu, Yesu
Khristu. Tikufuna tidziwe nchifukwa chani anabwera ku dziko la pansi. Tiphunzitseninso
kuchokera m'mau anu. Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.


Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:

Werengani gawo la Baibulo pansipa ndipo mulembe m'mau anu zimene limanena
za chifukwa chimene Yesu anabwerera ku dziko lapansi.

Mateyu 5:1-2, 17-20

Yohane 6:35-38

Machitidwe 2:23-24

1 Yohane 3:5-6

Aheberi 2:14-15

Chibvumbulutso 3:20-21

Chibvumbulutso 5:9-10

1. Chifukwa chani Yesu anabwera pa tdziko la pansi? Baibulo likutipatsa zifukwa
zambiri pansipa.

a. Mateyu 5:17

b. Yohane 1:18

c. Mateyu 20:28

d. Luka 4:42-43

e. Luka 19:10

f. Yohane 3:17

g. Yohane 10:7-10

h. 1 Timoteyo 1:15


“Yese wachimwa ndi kutalikilana ndi kupezeka kopulumutsa kwa
Mulungu.”

—Aroma 3:23

Chilango cha uchimo chinalengezedwa ndi Mulungu kwa Adamu ndi Hava pa chiyambi. Chilango chinali cha imfa ya kuuzimu ndi kuthupi. Genesis 2:17 ikuti, “Koma mtengo wa kudziwitsa chabwinio ndi choyipa musadye, pakuti tsiku limene mudzadya mudzafa."


“Pakuti tchimo lili ndi dipo lake—imfa; koma mphatso ya ulele ya
Mulungu ndi moyo wosatha mu ubale ndi Khristu Yesu Mbuye wathu.”
—Aroman 6:23

Yesu ndi mlowa malo wathu

Kuyambira ku Chipangano cha Kale, mulungu amavumbulutsa kuti mlowamalo
wosalakwa, wosachimwa afe chifukwa cha tchimo la wina. koma tangowerenga
Aroma 3:23, imene ikuti onse anachimwa. Sipanakhaleko munthu ochimwa,
kupatulako Yesu Khristu.

“Khristu analibe tchimo Christ . . . .”
—2 Akolinto 5:21

2. Yesu ananeneratu momveka bwino kuti adzaphedwa ndi kuuka kwa akufa.
Anawuza yani, ndipo anawawuza chani tikawerenga pansipa?

a. Luka 18:31-33

b. Mateyu 12:38-40

c. Marko 8:31-32a


3. Kodi adani a Mulungu akanampeza Iye olakwa? Luke 23:4

4. Poti Yesu sanachimwepo kapena kuphwanya lamulo lililonse, chifukwa chani
anaweruzidwa kuti afe. Marko 14:61-64

Yesu amadziwa zonse izi zidzachitika. Dzilko lisanalengedwe., Anakonza kubwera
ku dziko kufa ngati Mlowa malo wa munthu. Iyi inali njira yokhayo imene anthu
akanapulumutsidwira kuchoka ku zotsatira za tchimo. Yesu anadziwa mazunzo
amene amayenera kudutsamo.
5. Pa zomangidwa zonse, imfa, ndi kukwiriridwa kwa Yesu, kuyamba pa
Marko 14:43–15:47.

Izi zinalembedwa M'mauthenga Abwino onse anayi. Wolemba wina aliyense
akutsindika zinthu zosiyana malingana ndi m'mene amawonera. mu zolemba zina,
timaphunzira kunali ziweruzo zambiri chifukwa kunali kovuta kuti amuweruze pa
chinthu choyipa. Timaphunziranso zina zimene Yesu ananena pa mtanda.

Mateyu analemba zinthu kwa zimene anthu a Chiyu amafuna kumva (Mateyu 27:27–28:15). Analemba za boma kutumiza asilikali kukatseka manda. Mateyu akufotokoza izo zidzchitika pamene Yesu anawuka kwa akufa.

Yohane anakamba zambiri za anthu amene Yesu anakamba nawo atauka kwa akufa.Anafotokoza za boma kutumiza asilikali kukatseka ndi kulondera manda. (Yohane 19:16-21:25).

Luka analemba ma buku awiri, Uthenga wa Bwino wa Luka ndi buku la Machitidwe.
Mu ma buku onse. (Luka 23:26–24:52 and Machitidwe 1:1-11), anafotokoza za m'mene Yesu anatengedwera ku mwamba masiku makumi anayi atatha chiukireni kwa akufa.

6. Baibulo limaphnzitsa momveka bwino Yesu anabwera pa dziko ndi kufa m'malo mwako chifukwa cha machimo ako. poti Yesu anafa chifukwa cha iwe, yankho lanu lidzakhala lotani?


7. Lowezani Machitidwe 4:12.

Lembani Machitidwe 4:12 pano.

........................................................................................................................................................

8. Uzani ambuye kuti ndinu ayamika bwanji kuti Iye amakukondani ndipo
anakuferani pa mtanda kulipira dipo la tchimo lanu. Lembani pemphero lanu apa.

Pemphero Lotsekera

Tikuyamikani, Atate wa kumwamba, chifukwa cha chiplumutso munapereka kwa ife.
Zikomo chifukwa cha chikondi chanu . Tikuthokozani Atate kumwamba, chifukwa cha
chipulumutso mudapereka kwa ife. zikomo chifukwa cha chikondi chanu
chosasinthasintha pa ife ngat anthu. Tiphunzitseni tichite zonse mwatiphunzitsa pa moyo
wathu. Tapemphera mu dzina la mphamvu la Yesu Khristu, ame.

 
 

 

YESU NDI NDANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us