Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani? >>phunziro 1
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #1
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mulungu ali ngati chiyani?
Mulungu Ndi

Mulungu wakhala alipo,
Ndipo adzakhalapobe!
Kupezeka kwake kwa muyaya kumatchulidwa mwamphamvu
mmawu awiri kuti: -Mulungu Ndi.

Mulungu Wamphanvu zonze, opezeka paliponse nthawi ili yonse, amene amadziwa zonse, ali pano.

Adzakhalapobe, chifukwa - Mulungu Ndi.

“Koma opanda chikhulupiliro sikutheka kumkondweretsa, Pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupilira kuti alipo, ndikuti ali obwezera mphotho iwo akumfuna Iye
—Ahebri 11:6

1. Werengani Ahebri 11:6. Ndi liwu liti limene lagwiritsidwa ntchito pofotokozera kuti Mulungu Ndi?

Mulungu ndi Wolenga

Isanayambike nthawi, kunalibe kathu koma Mulungu yekha mu ukulu wake analipo. Kunalibe kanthu –kunalibe mlengalenga, kunalibe dziko, kunalibe dzuwa, kunalibe mwezi ngakhalenso nyenyezi – kunalibe kathu. Mulungu analankhula ndipo popanda kathu paja panabwera kanthu. Kulenga zinthu popanda zinthu.

Chikhalire-Mulungu ndi olenga ndipo palibenso wina,

2. Werengani mavesi awa ndipo mufotokoze mmene mukumvera (Mmmawu anu) choonadi chenicheni chimene mawu amenewa akuphunzitsa. (Mawu a mchipangano chakale akupezeka pamapeto pa phunziro liri lonse.)

Nehemiya 9:6

Akolose 1:15-16

Choonadi chenicheni chimene mavesi amenewa akuphunzitsa ndi:

Mulungu ndi wamuyaya

Mawu awiri aku "Mulungu Ndi” akutsimikitsa kuti Mulungu ndi wa Muyaya. Umuyaya ndiwovuta kumvetsa chifukwa cha nyengo imene tikukhala. Ndife akapolo a nthawi.

Nthawi imene tinabadwa inalembedwa mkawundula. Ndipo idzakhalaponso nthawi ya kufa, Zimene tikuchita tili ndi moyo, kuyambira pachiyambi mpaka pa kumapeto, zimayesedwa ndi nthawi monga zaka, masiku, maora ndi mphindi. Nthawi zonse timazindikiritsidwa za nthawi imeneyi. Choncho ndikovuta kuti timvetse zakukhala kunja kwa nthawi.

3. Werengani mavesi awa ndi kufotokoza mmene mukumvera choonadi checheni chimene mavesiwa akutiphunzitsa.

Masalimo 102:12, 25-27

Mulungu sayendera nthawi. Alibe chiyambi ndipo alibe mathero. Amakhala mu umuyaya. Sayendera nthawi.

Timakhala mnyengo zitatu - yammbuyo, yatsopano ndi yamtsogolo, Takhala nthawi yam’mbuyo, tikukhala nthawi yatsopano ndipo tidzakhala nthawi yamtsogolo, Mulungu analipo chikhalire ndipo adzakhalapo mpaka kale.

Mulungu m'modzi yekha

4. Werengani mavesi awa ndipo yankhani funso lotsatilari. Kodi mukukhulupilira kuti kuli Mulungu mmodzi? Perekani chifukwa mmene mwayankhira.

Yesaya 44:6

Yesaya 45:5

Kodi Baibulo ndi loona?

Mabuku ena a m’baibulo analembedwa ndi aneneri. Awa ndi azitukimiki amene ankanena uthenga wa Mulungu kwa anthu. Amanena zimene zidzachitike mtsogolo ngakhale zaka zochuluka mtsogolomo.

Cholinga cha uneneri mu Baibulo nkutidziwitsa kuti Mulungu alipo ndipo ali ndi cholinga pa dziko lino ngakhalenso anthu. Pakunenera za anthu, malo, ndi zochitika zaka za mtsogolo, Mulungu amakhala akutidziwitsa za cholinga chake pa dziko mtsogolomo. Kupherezera kwa uneneri ndi chitsimikizo kuti Baibulo ndi mawu a Mulungu

5. Baibulo limaonekera kudalirika pakuwona kupherezera kwa uneneri.

Mneneri Mika ananenera za malo obadwira a Ambuye Yesu zaka 700 Ambuye Yesuwo asanabadwe.

Mika 5:2
“Koma iwe, Betelehemu Efrata,
ndi iwe wamng’ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda,
mwa iwe mudzanditulukira
wina wakudzakhala woweruza m’Israyeli;
maturukiro ace ndiwo a kale lomwe,
kuyambira nthawi yosayamba”

Uneneri uwu unakwaniritsidwa pa Mateyu 2:4-6.

Kodi Ambuye Yesu anabadwira kuti? ……

Munthawi yayikulu mchiyembekezero cha Ambuye Yesu, Maria amakhala kumpoto kwa Israyeli ku Nazarete. Betelehem anali kum’mwera kwa Israyeli. Koma boma la a Aroma linalamula kalembera. Aliyense amayenera kubwelelera kwa makolo ake kukalembetsa. Yosefe ndi Maria anali ochokera banja la chifumu la Davide omwe kwawo kunali ku Betelehemu – (1 Samueli 16:1). Malemba anakwaniritsidwa Ambuye Yesu anabadwira ku Betehemu osati ku Nazarete. Ndi Mulungu yekha amene amapanga zithu kutheka. Mulunguyo anatheketsadi.

6. Davide ananenera za kupachikidwa kwa Ambuye Yesu zaka
chikwi Ambuye Yesu aasanabadwe.

Mwachitsanzo, Werengani

Masalimo 22:18
“Agawana zovala zanga, Nalota maere pa Malaya anga.”

Uneneriwu unakwaniritsidwa pa Yohane 19:23-24.

Kodi asilikali aja anapanga chiyani?

Uneneri uwu unakwaniritsidwa ndi asilikali a chi Roma amene sanadziwa nkomwe za uneneri wa Chiyuda. Sanakatha kulumikiza ndi munthu amene anangompachika kumene. Ndi Mulungu yekha amene anakanenera zimenezi ndikudziwitsa kuti uneneriwu wakwaniritsidwa.

7. Fotokozani mwachidule zimene Ambuye Yesu ananena zokhudza chipangano chakale. Luka 24:27, 44

8. Kodi pa 2 Timoteo 3:16 pakuti chiyani za m’mene Baibulo limatitakasira miyoyo yathu?

9. Kodi mawu akuti Mulungu Ndi akutanthauza chiyani kwa inuyo pamene mwamaliza phunziro limeneli? …

Pemphero
Ambuye Mulungu. Ndayamba kuwona ukulu wanu. Ndithandizeni kuzindikira chimenechi, ngakhale kuti sindingakudziwitsitseni, Inu mukufunitsitsa nditakudziwani. Pitirizani kundiphunzitsa ndi kundithandiza kusunga choonadi chimene ndikuwerenga lero. Mudzina la Yesu ndapemphera. Amen

Pemphero
Atate wa muyaya. Ndikukupembedzani. Ndaphunzira kuti mulibe chiyambi ndiponso mulibe mathero. Ndikuvomereza kuti inu ndi wolenga wamkulu ndipo palibenso wina. Ndikupempha kuti mundithandize kuganiza bwino za Inu pamene ndikuwerenga mawu anu. Ndapempha izi kudzera mudzina la Yesu Khristu. Amen

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us