Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani? >>phunziro 1 >>phunziro 2
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #2
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mulungu ali ngati chiyani?

Prayer

Eternal Father, I worship You. I have learned that You had no beginning and will have no end. I acknowledge You as the great Creator of all that exits. I ask You to help me think correctly about You as I read Your Word. I pray in the name of Jesus. Amen

1. Pogwiritsa ntchito mawu anu (Mwachindunji). Fotokozani za m’mene mukuganizira kapena kuwonera mukamaganiza za Mulungu. Munene mwachilungamo komanso mwatchutchutchu m’mene mumaganizira za Mulunguyo. Pakutha pamaphunzirowa, funsoli lifunsidwanso.

Kuwerenga Baibulo sabata ndi sabata

Tsiku lirilonse msabatayi, werengani vesi la lomwe mwapatsidwa patsiku, mchipangano chatsopano ndipo munene zam’mene mawuwo akukambira za Muliungu.

1 Akorinto 1:9
Kodi vesi limeneli likunena chiyani za Mulungu? …

Aroma 16:27
Kodi vesi limeneli likumufotokoza bwanji Mulungu?

Luka 1:37
Kodi vesi limeneli likuti chiyani za Mulungu?

Yohane 3:16
Kodi vesi limeneli likufotokoza chiyani za Mulungu?

Numeri 23:19
Ndi ubwino wanji wa Mulungu umene ukufotokozedwa pamenepa?

Chivumbulutso 15:3-4
Ndi ubwinonso wanji wa Mulungu umene ukufotokozedwa?

Chivumbulutso 1:8
Kodi apa mawu akuti chiyani za Mulungu?

*Sankhani vesi m’baibulo limene tawerenga msabatayi limene lakukhudzani kwambiri komanso liri ndi tanthauzo pa moyo wanu nthawi ino. Ganizirani tanthauzo la choonadichi kwa inu ndipo muligwritse ntchito pa moyo wanu.

Mulungu sawoneka mu thupi. Ife anthu timaganiza molakwikwa poyesa kuti Mulungu amawoneka ndi maso komanso ali ndi malire pochita zinthu monga ifeyo.

Ife sitinadzipezeketse tokha padziko lino, kapena kulenga mpweya, chakudya ngakhalenso madzi zomwe zimafunikira kuti munthu akhale ndi moyo. Komatu Mulungu alipo wathunthu mu Umulungu wake. Sakusowa wina wake kapenanso china chirichonse kuti Iyeyo apezeke koma Iye yekha mwa yekha.

Chiri chonse chomwe timachiwona mdziko lino chinalengedwa kapena kukonzedwa koma Mulungu sanalengedwe kapenanso kukonzedwa. Mulungu ndi wosiyana ndi chirichonse. Dzina lake ndi NDI INE. Aliko ndipo analipo. Iyeyu ndi wa muyaya. Sadzakkhala ndi mathero.

Chimene chimatisiyanitsa ndi chakuti ife ndi ife anthu ndipo Mulungu ndi Mulungu ndipo ali ndi Umulungu sawoneka ndi maso koma ifeyo timawoneka ndi maso.

2. Kodi Yohane 4:24 imanena chiyani za Mulungu? ……

Mulungu wathu alibe malire

“Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi m’Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa zotani nanga nyumba iyi ndayimangayi!”
1 Mafumu 8:27

“Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna?
Ukhoza kupeza Wamphamvu yonse motsindika?
Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji?
Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji? Muyeso wake utalikira utali wache wa dziko lapansi, Chitando chake chiposa Nyanja. “
Yobu 11:7-9

Mulungu ndi osamvetsetseka

“Mulungu agunda modabwitsa ndi mawu ake, Achita zazikulu osazidziwa Ife”
Yobu 37:5

“Pakuti maganizo anga Sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitali, kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.”
Yesaya 55:8-9

3. Ukoma wa Umulungu ndi ubwino umene uli owona pofotokoza za
Mulungu. Mavesi ali munsiwa ali ndi ukoma wa umulungu. Werengani ndi kulemba ukoma wa vesi ili yonse.
a. 1 Yohane 4:8 …
b. 2 Atesolonika 3:3 . . . .
c. Yakobo 1:17 . . . .
d. Yakobo 10:18 . . . .
e. Ahebri 1:8 . . .
f. Luka 1:78 . . . . .
g. 1 Petro 1:15-16 . . . . .

UKOMA WA MULUNGU

Mulungu ndiChikondi

Chikondi ndiukoma kapena kuti ubwino wa Mulungu koma sichitanthauza Mulungu.

Mulungu ndiye amamasulira kuti chikondi ndi chiyani. Koma chikondi sichinena kuti Mulungu ndi chiyani kapena kuti ndi ndani? Chikondi chimangofotokoza momwe Mulungu aliri monganso m’mene ma ubwino ena a Mulungu akufotokozera. Kukhulupirika, kukoma mtima, chifundo, chilungamo komanso chiyero zimafotokozera ubwino ndi cholinga chimene Mulungu amapezekera. Amakhala mu zonsezi nthawi ili yonse. Chikondi cha Mulungu ndi choyera nthawi zonse, ndi chabwino nthawi zonse, ndi chokhulupilika nthawi zonse, ndi chachifundo komanso ndi choonadi.

Mulungu ndi okhulupirika

Titha kudalira Mulungu chifukwa Iye ndi okhulupilika. Amasunga malonjezano ake. Titha kukhala mchiyembekezo mtsogolo chifukwa kukhulipilika kwa Mulungu sikulephera.

Mulungu sasintha

Umodzi mwa ubwino wa Mulungu umene sitidautchule ndi wakuti Iyeyu sasitha. Tikudziwa bwino lomwe kuti Mulungu sangakhale osakhulupilika chifukwa zikatero akuyeneranso kusintha. Mulungu ndi wolungama komanso sangalephere. Werengani Malaki 3:6

Mulungu ndi wabwino

Ubwino wa Umulungu ndi osiyana ndi ubwino wa umunthu. Izi ziri chomwechi chifukwa Mulungu ali olondola muzake zones komanso nthawi ili yonse. Yesu anati: - Ndi Mulungu yekha amene ali wabwino? Werengani Masalimo 107 vesi 1

Mulungu ndi Wachilungamo

Mulungu akamapanga chilungamo, samapanga mofuna kulingana ndi chilungamo cha munthu. Iye amapanga zimene iye amadziwa. Mulungu ndi Mulungu ndipo adzakhala Mulungu ndipo sangakhalenso chiri chonse. Iye ndi Mulungu basi. Ndi wa chilungamo. Werengani Deutoronomo 32 Vesi 4

Mulungu ndi wachifundo

Chifundo ndiubwino wa Mulungu. Amakhudzidwa, ndiwachifundo nthawi zonse komanso ndi wachilungamo. Ngakhale pamene akuweruza amachita chifundo. Amamchitira munthu chifundo mosatopa. Chifundo cha Umulungu sichalero kapena mawa lokha koma ndi ubwino wa Mulungu wa muyaya. Mulungu ndi wachifundo kuyambira kale ndipo ndichopitilira mpaka muyaya.
Werengani 2 Akorinto 1:3

Mulungu ndi Woyera

Kuyera kwa Umulungu ndi kwachikhalire. Ndi kwapadera, kosafikilika, kosapezeka komanso kovuta kukumvetsa. Mulungu ndi opanda banga ndi umoyo wake ndi wangwiro. Ubwino wa Umulungu wa chiyero ndi wapaderadera kwa Mulungu.

4a. Kodi Mulungu amayembekezera chiyani kuchokera kwa aKhristu?
1 Petro 1:13-16

b. Malinga ndi 1 Akorinto 1:30, Kodi tingakhale bwanji woyera? . . . . .

Atero Yehova wanzeru “Asadzitamandire m’nzeru zache,
wamphamvu asadzitamandire m’mphamvu yache,
wa chuma asadzitamandire m’chuma chache;
Koma wakudzatamandira adzitamandire adzikweze umo,
kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wochita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi, pakuti m’menemo ndikondwera, atero Yehova.”
Yeremiya 9:23-24

Ubwino utatu wapaderadera

Mulungu ndi wamphamvu zonse. Analenga dziko ndi zonse zam’dzikoli ndi mawu. Amaliramulira. Ali ndi mphamvu yochita zozizwa. Choncho titha kunena kuti Mulungu ndi wamphamvu zonse.

Mulungu amadziwa chirichonse. Palibe chimene sadziwa. Mphamvu za Mulungu ndi nzeru zake ndi zophatikizana ndipo palibe angazipatule. Choncho timamutcha Mulungu wa nzeru zonse.

Mulungu amapezeka paliponse nthawi imodzi. Choncho timamutcha Mulungu opezeka paliponse.

5. Werengani mavesi otsatirawa ndipo mulembe ma ubwino atatu apaderaderawa malinga ndi vesi ili yonse momwe iliri – Mulungu ndi Wamphamvu yonse, Opezeka pali ponse ndiponso Wanzeru zakuya.

“. . . Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.”
Mateyu 28:20

“. . . Ine ndine Mulungu Wamphayonse . . . Kodi chiripo chinthu chomulaka Yehova?”
Genesesi. 17:1; 18:14

“Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pache, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pache pa Iye amene tichita naye.”
Ahebri 4:13

Pemphero
Mulungu wa mphamvu zonse, Zikomo chifukwa cha zonse zimene ndaphunzira zokhudza inu. Zikomo chifukwa mukupezeka pali ponse, chifukwa ndi Inu wamphamvu zonse, ndipo mumadziwa chirichonse. Ndi Inu Mulungu odabwitsa. Ndiine okondwa kuti mumakonda ndi kumvetsetsa anthu omwe munawalenga. Ndikukuwezani chifukwa cha chakutidalitsa. Mudzina la Yesu Khristu, amen

 

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us