Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani? >>phunziro 3 >>phunziro 4
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #4
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kodi Mulungu amandidziwa?

Pemphero
Atate wamuyaya, Zikomo pondiuza za Inu kudzera m’Baibulo. Ndithandizeni kuti ndikukhulupilireni kuti mukumane ndi zosowa za moyo wanga wa tsiku ndi tsiku. Thandizeni kuti ndimvetse kuti muli ndi cholinga ndi moyo wanga. Ndapemphera mdzina la Yesu Khristu. Amen.

Kuwerenga Baibulo sabata ndi sabata

Tsiku ndi tsiku msabatayi, werengani Baibulo malo amene mwapatsidwa kuti muwerenge ndipo muyankhe funso lotsatirali.

Yohane 6:37
Ndi chiyani chodziwikiratu, chimene mungachipeze mukabwera kwa Yesu?

Yobu 34:21
Ndi zingati zimene timapanga zomwe Mulungu amaziwona?

Masalimo 139:1-4
Kodi ndime zimenezi zimanena bwanji zam’mene Mulungu amadziwira anthu?

Miyambo 15:3, 11
Mumadziwa bwanji kuti Mulungu amadziwa malingaliro anu?

2 Mbiri 16:9
Kodi Mulungu akufuna chiyani?

Hebrews 13:5
Kodi Yesu adzakusiyani liti?

Yohane 14:21
Kodi kumukonda ndi kumvera Mulungu zimakhudzana bwanji? Nanga Mulungu amaziwona bwanji?

* Sankhani vesi imodzi mwamavesi amene mwawerenga kuchokera mu Baibulo msabatayi, imene yakugwirani mtima panthawi ino. Ganizirani tanthauzo la vesi imeneyi kwa inu ndipo kuti mungayigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanu?

1. Kodi fanizo lomwe likupezeka pa Mateyu 18 vesi 12 mpaka 14 likunena chiyani za mmene Mulungu amawonera Munthu aliyense.

2. Ephesians 2:10
Kodi ndime imeneyi ikutiphunzitsa chiyani za zomwe Mulungu wachitira munthu aliyense?

3. Pamene ndikuzama pakumdziwa Mulungu, ndikuphunzira zinthu zinthu zotsatirazi:
Mulungu ali ngati chiyani? — Buku lophunzilira

4. Masalimo 139:1-18 ndi chitsimikizo kuti Mulungu amamudziwitsitsa munthu. Pamene mukuwerenga Masalimowa, lembani ndime zimene zikukugwirani komanso kuthunzitsa mtima wanu.

5. Werengani pemphero lomwe liri pa Masalimo 139:23-24 ndipo lembani pemphero lanu pogwiritsa nzeru za mndime zimene mwawerengazi.

Encourage the group by having each person read his or her prayer, if time allows.

6a. Mulungu amakudziwani ndipo amadziwa zonse zanu komanso amadziwa zosowa zanu. Kodi pali kanthu kokudandaulitsani? Mateyu 6:25-34

b. Kodi Mulungu akufuna kuti inu mutani ndi zinthu zimene zimakudandaulitsani? 1 Petro 5:6-7

c. Kodi ndi nthawi yanji imene Mulungu amadziwa kuti mukusowa ndipo mukufuna kanthu pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Mateyu 6:8

7. Kuti mumudziwe Mulungu bwino, pezani lonjezano lake mundime zamchipangano chakale zotsatirazi zomwe ziri kumapeto kwa phunziro liri lonse.
Masalimo 37:4-5

Miyambo 3:5-6

Yeremiya 29:13

8. Lingalirani za mtsogolo za moyo wanu. Kodi malonjezanowa angakhudze bwanji za kukonzekera tsogolo lanu?

9. Kodi Mulungu ali ndi cholinga chanji ndi tsogolo lanu?
Werengani Yeremiya 29:11

10. Pakuti Mulungu amakudziwani monga munthu. Iye wasonyeza chikondi chake pa inu ndipo wakupangirani zinthu za kuti inuyo panokha simunakatha kupanga.

Molingana ndi Aroma 5:6-9, kodi Mulungu anakupangirani chiyani?

11. Pamene tikapereka miyoyo yathu kwa Mulungu Wamphamvuyonse, ndi chifukwa chiyani tiyenera kukhulupilira kotheratu kuti tiri otetezeka?
Werengani Masalimo 147:5

12. Lembani pemphero kwa Mulungu, kufotokoza mwa chiyamiko kuti Iye ndi Mulungu odziwa zonse. Pempheroli simufunsidwa kugawana ndi anzanu pophunzitsana Baibulo. Lembani pemphero lanulo panopo.

Pemphero
Heavenly Father, how we thank You that You know all about us and You still love us. Thank You for the perfect plan You have for our lives. Help us make the things we have learned a part of our daily living. We pray in Jesus’ name, amen.

Mawu a m’Baibulo a Chipangano Chakale-
Buku Lopatulika ndilo Mawu a Mulungu.

Yobu 34:21
Pakuti maso ake ali panjira ya munthu aliyense, Napenya moponda mwache monse.

Masalimo 139
1 Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa
2 Inu mundidziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, Muzindikira lingaliro langa muli kutali.
3 Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njra zanga zonse muzolowerana nazo.
4 Pakuti asanafike palilime langa, tawonani, Yehova, muwadziwa onse.
5 Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunayika dzanja lanu pa ine.
Mulungu ali ngati chiyani? — Buku lophunzilira
6 Kudziwa ichi kundilaka ndikundidabwitsa: Kundikhalira patali. Sindifikirapo.
7 Ndidzapita kuti kuzembera Mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu.
8 Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadzayalira ku gehena, tawonani, muli komweko.
9 Ndikadzitengera mapiko a m’bandakucha, ndi kukhala kumalekezero a nyanja;
10 Kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, niridzandigwira dzanja lanu lamanja.
11 Ndipo ndikati, koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga ukhale usiku;
12 Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika.
13 Pakuti Inu munalenga ipso zanga; munandiwumba ndisanabadwe.
14 Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsya nchodabwitsa; ntchito zani nzodabwitsa; Moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
15 Thupi langa silinabisikira inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga munsi mwake mwa dziko lapansi.
16 Ndisanawumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu, masiku akuti ziwumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.
17 Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu zamtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri!
18 Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.
19 Indedi, mudzawomba oyipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine.
20 Popeza anena za Inu moyipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.
21 Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuwukira inu?
22 Ndidana nawo ndi udani weniweni: ndiwayesa adani.
23 Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga;
Mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.
24 Ndipo mupenye ngati ndiri nawo mayendedwe oyipa.

Miyambo 15:3, 11
Mulungu ali ngati chiyani? — Buku lophunzilira
3 Maso a Yehova ali ponse ponse, nayang’anira oyipa ndi abwino.
11 Kumanda ndi kuchiwongeko kuli pamaso pa Yehova; Koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?

2 Mbiri 16:9
Pakuti maso a Yehova ayang’ana uku ndi uku ku dziko lonse lapansi, kudziwonetsera wa mphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m’menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzawona nkhondo.

Masalimo 100:3
Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa za pa busa pake.

Masalimo 37:4-5
Udzikondweretsenso mwa Yehova;
Ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiliranso Iye, adzachichita

Miyambo 3:5-6
Khulupilira Yehova ndi mtima wako onse
Wosachirikizika pa luntha lako;
Umulemekeze mnjira zako zonse,
ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.

Yeremiya 29:13
Ndipo mjudzandifuna ine, ndikundipeza,
pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

Yeremiya 29:11
Pakuti ndidziwa malingiliro amane ndilingililira inu,
Ati Yehova, malingiliro a mtendere, si a choyipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.

Masalimo 147:5
Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wamphamvu zambiri; Nzeru yake njosatha
Mulungu ali ngati chiyani? — Buku lophunzilira

 

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us