Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani? >>phunziro 4 >>phunziro 5
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #5
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Oyenera kumdziwa Mulungu Ndani?

Pemphero
Atate, ndikufuna kudziwa zambiri za Inu. Ndithandizeni kuti ndimvetse zinthu zimene ndikuwerenga. Mwandizizwitsa pakuti zolengedwa zonse ziri pansi panu koma ngankhale ziri choncho mukufuna kuti ine ndikhalebe bwenzi lanu. Ndapemphera mu dzina la Yesu. Amen.

Mulungu sayembekezera kuti tidziwe zonse za Iye, koma amafunitsitsa aliyense adziwe zoonadi zake izi:

  • Mulungu ndi m’modzi, amapezeka mu Utatu: Mulungu Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera
  • Mulungu Atate ndi Mzimu wa Umulungu.
  • Yesu Khristu anabwera padziko lapansi mu Umulungu wake kudzakhala munthu.
  • Ngati Munthu, anakhala pano pa dziko lapansi ndi moyo wangwiro.
  • Anafera pa mtanda, anayikidwa m’manda ndipo anawuka kwa akufa.
  • Atauka, Anabwelera kumwamba mu thupi lake la ulemelero.
  • Mulungu Mzimu Oyera ndi wosaoneka ndi maso, koma ali nafe limodzi panopo.
    Mulungu amatidziwa. Amatidziwa bwino kuposa aliyense. Wakhala akutidziwa. Funso nkumati – Kodi mumamudziwa Mulungu?

God knows us. He knows us better than anyone else. He has always know us. the question is - do you know God?

Kuwerenga Baibulo m’sabata

Tsiku liri lonse m’sabata, werengani malo amene mwapatsidwa m’Baibulo kuti muwerenge ndi kuyankha funso lotsatira:

Yohane 14:21-23
Kodi Mulungu adzadziwululira kwa yani?

Aroma 5:6-9
Ndi chifukwa chiyani Yesu anatifera pamene tinali ochimwa?

1 Timoteo 2:1-6
Ndi ndani amene Yesu akufuna apulumutsidwe?

Yakobo 4:7-10
Kodi Mulungu amafuna kuti titani kuti Iye akhale pafupi nafe?

2 Petro 3:9
Ndi chifukwa chiyani Mulungu akuchedwa kuweruza dzikoli?

Ahebri 11:6
Mukafika pamaso pa Mulungu, kodi muyenera kukhala ndi chikhulupiliro chotani?

Mateyu 11:27-30
Kodi Mulungu amayitana ndani kuti afike kwa Iye?

* Sankhani ndime imodzi mwa ndime zimene mwawerenga kuchokera mu Baibulo msabatayi, imene yakugwirani mtima panthawi ino. Ganizirani tanthauzo la ndime imeneyi kwa inu ndipo kuti mungayigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanu?

1. Kodi Baibulo limati Chiyani za m’mene munthu angamdziwire Mulungu?

Masalimo 46:10

Masalimo 145:18-19

Yesaya 55:3

Ahebri 10:22

2. Yesu anauza ophunzira ake za m’mene angamudziwire Mulungu. Werengani Yohane 14:6-7 Ndipo mufotokoze zimene anawawuza.

Mulungu amadziwa kuti ndife ochimwa. Amadziwa kuti sitingadzimasule tokha ku tchimoli. Pa Aroma 3:20-24 Baibulo limatiuza momwe tingamasukire ku tchimo.

Liwu lakuti - khulupilira” silikungotanthauza za kuti Yesu Khristu ndi mwana wa Mulungu, amene anapachichikidwa pantanda chifukwa cha machimo anu. Mawuwa akutanthauza kuyika mtima wanu wonse ndi kumudalira Yesuyo pakulapa machimo anu.

Kulapa ndi kusintha njira ndi kulondola Yesu Khristu. Izi zikutanthauza kuti simuyenera kuyenda njira yanu. Kulapa kumatanthauza kusiya njira zanu zakale ndi kulondola Mulungu.

Kodi mwalandira mphatso ya Mulungu ya chipulumutso?

Ngati mulibe Yesu m’moyo wanu, lankhulani ndi Mulungu mu pemphero, lapani machimo anu, pemphani akukhulukireni nakupatsani moyo wosatha.

Mulungu akukhululukirani chifukwa chikhululukiro komanso moyo wosatha ndi mphatso zimene Iye akufuna kukupatsani. Mphatso izi sizokuyenerani koma mukungoyenera kukhulupilira ndi kuzilandira.

3. Werengani mavesi otsatirawa. Kodi tipange chiyani kuti tilandire mphatso kuchokera kwa Mulungu?

Yohane 6:29

Yohane 5:24

4. Yesu anauza munthu kuti ayenera kubadwanso mwatsopano. Werengani Yohane 3:1-8 kuti mumve zimene Yesu ananena zakubadwira m’banja la Mulungu?

Lembani tsiku kapena zaka zanu pamene munamkhulupilira ndi kumulandira Yesu kukhala Mbuye ndi Mphulumutsi wa moyo wanu.

5. Pamene munkapemphera, kuti Yesu alowe mumtima mwanu, zambiri zodabwitsa zinachitika. Talembani madalitso amane ndime zotsatilazi zikutiwululira.

a) Yohane 3:36

b) Yohane 16:24

c) Aroma 4:7-8

d) Aroma 5:1

e) 2 Akorinto 5:17

f) Aefeso 1:13

g) Ahebri 13:5

6. Lembani pemphero lanu kwa Mulungu, kumuthokoza pokudziwani ndi pokuwonetsani njira ya m’mene mungakhalire pa ubwebnzi ndi Iye. Mupepmpheni kuti akhale nsanamila yanu nthawi zonse. Pa nthawi imene mukuphunzira mwa kukambirana, mutha kugawana pemphero lanu ndi anzanu.Lembani pemphero lanu pano.

Pemphero
Father in Heaven, we thank You for Your gift of salvation. Thank You for making it possible for us to receive all the blessings You have for Your children. As we study our last lesson, help us learn how to live to please You. We pray in Jesus’ name, amen.

Mau a mchipangano chakale

Yeremiya 29:13
Ndipo mudzindifuna Ine ndi kundipeza pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse

Masalimo 46:10
Khalani chete, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu:
Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.

Masalimo 145:18-19
Yehova ali pafupi ndi onse akuyitanira kwa Iye,
Onse akuyitanira kwa Iye mchoonadi.
Adzachita chokhumba iwo akumuwopa;
Ndidzamva kufuula kwawo nadzawapulumutsa.

Yesaya 55:3
Tcherani khutu lanu, mudze kwa ine, imvani, mzimu nudzakhala ndi moyo;………….

Ezekieli 18:32
Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova, chifukwa bwelerani, nimukhale ndi moyo.

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us