Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani? >>phunziro 5 >>phunziro 6
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #6
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Ndingamkondweretse bwanji Mulungu?

Pemphero
Atate, Zikomo chifukwa cha zonse zimene ndaphunzira zokhudza Inu. Ndikudziwa kuti sindingamvetsetse za ukulu wanu, chifukwa zifundo zanu ndizochuluka ndipo munthu sangazimvetse. Mudzina la Yesu Khristu ndapemphera. Amen

Kuwerenga Baibulo m’sabata

Tsiku liri lonse msabatayi, Werengani Baibulo malo amene mwapatsidwa ndipo yankhani funso lotsatirali.

Mariko 12:28-31
Nenani mwachidule malamulo awiri a Mulungu aakulu

Mateyu 4:10
Kodi tiyenera kupembedza ndi kutumikira yani?

Mateyu 12:50
Kodi ndi chiyani chimene chimawonetsera kuti tiri pa ubale weni weni ndi Yesu?

Yohane 14:23
Mumawonetsera bwanji kuti mumamukonda Mulungu?

Afilipo 1:9-11
Kudzachitika chiyani pamene mukusankha zabwino?

1 Akorinto 10:31
Kodi mungadzetse bwanji ulemelero wa Mulungu?

1 Mbiri 16:23-29
Kodi vesi 29, ikuti anthu adzipanga chiyani?

* Sankhani ndime imodzi mwa ndime zimene mwawerenga kuchokera mu Baibulo msabatayi, imene yakugwirani mtima panthawi ino. Ganizirani tanthauzo la ndime imeneyi kwa inu ndipo kuti mungayigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanu?

1. Mulungu wadziulula Yekha kwa anthu mu njira zisanu:
Mawu ake, umboni kuchokera kwa okhulupilira okhulupilika,

Chilengedwe chake,

chikumbumtima komanso

Yesu Khristu mwana wake.

Werengani mavesi otsatirawa ndipo potengera m’ndandanda walembedwa pamwambapa, sankhani njira imene Mulungu wadziululira yekha kwa ife.

Aroma1:20

2 Petro 1:20-21

Yohane 1:18

Machitidwe 1:8

1 Timoteo 1:19

Ubwino wa Mulungu kwa paderadera

Ubwino wina wa Mulungu ndi wapaderadera mu Umulungu wake. Palibe yemwe angakhale ngati Iye. Mulungu ndi:

Wodziyimira komanso wodzipezeketsa yekha.

Wamphamvu zonse

Wopezeka pali ponse

Wanzeru zakuya

Wa ulamuliro wangwiro komanso wopanda malire

2. Ubwino wina wa Mulungu ndi wapaderadera palibe wina angakhale nawo koma Iye yekha. Komanso ulipo ubwino wina umene Mulungu ali nawo ndipo amagawirako anthu mwa mlingo.

a. Werengani mavesi zotsatirawa ndipo mutchule ma ubwino amene Mulungu amagawana ndi munthu.

1 Yohane 4:16

Masalimo 107:1

Masalimo 86:15

2 Petro 3:15

Mateyu 6:14

Mateyu 11:29

Afilipo 4:7

b. Potengera ma ubwino amene mwalemba pa funso 2a, perekani zitsanzo za momwe mungawonetsere makhalidwewa pa moyo wanu tsiku ndi tsiku.
Mulungu ndi Oyera

3 a. Kodi ndi lamulo liti limene Mulungu watipatsa pa 1 Petro 1:16?

b. Chingakoke mtima wanu ndi chiyani kuti muyesetse kuti ubwino umenewu uwonekere pa moyo wanu? Ahebri 12:14.

4. Fotokozani mwachidule m’mene mumaganizira kapena m’mene mumawomera mukamaganizira Mulungu. Yankhani mwatchutchu komanso moona za m’mene mumadziwira Mulunguyo.

5. Werengani ndime zotsatirazi ndipo ndi mawu ochepa lembani chimene Mulungu akufuna kuti inu muchite.

Yohane 13:34-35

Yohane 14:15

Aroma 12:1

Aroma 12:2

1 Atesolonika 4:3

1 Atesolonika 5:16-18

Musanapange chiganizo, tayambani mwadzifunsa mafunso awa

Kodi ndikapanga ichi, chimkondweretsa Mulungu?
Chithandiza?

Kapena chibwezeretsa m’mbuyo ubale wanga ndi Mulungu?

Kodi chisankhochi chiwonetsera chikondi changa pa Mulungu?

Kodi chidziwitsa ena kuti ineyo ndimamukonda Mulungu?

Kodi ndiri ndi njala yochita chifuniro changa kuposa kuchita chifuniro cha Mulungu?

Masalimo 25:4-5. Kumbukirani kuti njira za Mulungu sinjira zathu. Funitsitsa kupanga zonse zimene Mulungu akukuwululirani ndipo adzakuwonetserani cholinga chake pa inu.

6.Poganizira zimene mwaphunzira, nenani zinthu zitatu kapena zinayi zimene mukufuna mutapanga kuti mumkondweretse Mulungu.

Kodi Mulungu angatipatse Moyo wake? Moyowu tingawulandire pokhapokha titakhala ndi mtima wodzichepetsa. Pamenepo mtima wa phindu ndi wodzipereka umenewu ungadzetse ulemelero pamaso pa Mulungu.

Ngati akhristu tikuyenera kudzifunsa kuti:

Kodi moyo wanga umawonetsera choonadi cha Mulungu?
Kodi Moyo wanga umawonetsera chikondi cha Mulungu?
Kodi moyo wanga umawonetsera chipiliro cha Mulungu?
Kodi ndimakhululuka ngati Mulungu amakhululukira?
Zinthu zoyenera pa kuyenda mu ulemelero wa Mulungu ndi kudzipereka komanso kumusangalatsa Mulunguyo. Tsiku liri lonse monga akhristu, tikuyenera kuwonekera kuti Mzimu wa Mulungu akugonera mwa ife.

Pamene moyo wathu watsiku ndi tsiku ukufotokoza kuti Mulungu ali ngati chiyani, Mulunguyo amagwitilitsa ntchito pofikira ena ndi kubweretsa ulemelero kwa Iye.

7a. Kodi ndi chifukwa chiyani Mulungu analenga Munthu? Yesaya 43:7

b. Kodi tingadzetse bwanji ulemelero kwa Mulungu? Yohane 15:8

8. Lembani pemphero, kumupempha Mulungu kuti akuthandizeni kugwiritsa ntchito zinthu zimene mwaphunzirazi. Muthokozeni chifukwa cha lonjezano lake lakukhala nanu mpaka muyaya. Mutha kugawana pempheroli ndi anzanu ngati mukufuna. Lembani panopo.

Haleluya!
Lemekezani Mulungu m’malo ake oyera;
Mulemekezeni mthambo la mphamvu yake.
Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba;
Mlemekezeni monga mwa ukulu wake wa unyinji!
Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.
Haleluya

Masalimo 150:1-2, 6

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us