Project Hope     home >>stonecroft>> mulungu ali ngati chiyani? >>phunziro 2 >>phunziro 3
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #2
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kodi Mulungu ali kuti?

Pemphero
Mulungu wa mphamvu zonse, ndikufuna ndiphunzire zambiri za Inu.
Ndithandizireni kumvetsetsa ndikudziwa zambiri za Inu pamene
ndikuwerenga mawu anu tsiku ndi tsiku. Ndidziwe kopezeka kwanu
ndikayitanira pa Inu. Ndapemphera mudzina la Yesu Khristu. Amen

Kuwerenga Baibulo sabata ndi sabata

Tsiku liri lonse msabatali werengani mawu a m’baibulo a tsiku liri lonse
ndi kuyankha funso lotsatira

Masalimo 34:18
Mulungu amapezeka kuti mukamufuna?

Masalimo 103:19
Mpando wachifumu wa Mulungu uli kuti?

Masalimo 145:18
Kodi ndime imeneyi ikutiwuza chiyani za Mulungu?

Yesaya 37:16
Ndime imeneyi ikuti Mulungu amakhala kuti?

Yesaya 40:22
Kodi ndime imeneyi ikutiwuza chiyani za komwe kuli Mulungu?

Yesaya 43:2
Mulungu amakhala ali kuti pamene muli m’mavuto?

Yeremiya 23:23
Mulungu amati ali kuti nthawi zonse?

* Sankhani vesi imodzi mwamavei amene mwawerenga kuchokera mu Baibulo msabatayi, imene yakugwirani mtima panthawi ino. Ganizirani tanthauzo la ndime imeneyi kwa inu ndipo kuti mungayigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanu?

1. Kodi Mulungu amakhala kuti? 1 Timoteo 6:16

Ndikovuta kumufikira Mulungu chifukwa cha kuwala kwa chiyero ndi kupanda banga kopambana kwache. Sikophweka kukhala pamaso pake chifukwa tikudziwiratu kuti ndi ife ochimwa. Koma chifukwa kuti Mulungu amadziwa kuti sitingafanane ndi chiyero chake, amadziwulura yekha kwa ife mu njira yakuti timumvetse. Mwachitsanzo maina ake amawulura za chimene Iye ali.
Timaphunzira kusunthira kufupi ndi Mulungu kudzera mu buku lomwe Iye analemba – Baibulo.

2. Kodi baibulo limati chiyani za komwe Mulungu sakhalako?
a. Machitidwe 17:24-25

b. 1 Mafumu 8:27

3. Ngati Mulungu amakhala malo owala kwambiri ovuta kufikako ndipo sakhala mzinyumba kapena m’matchalichi, kodi ndime ya 1 Yohane 4:12 imati padziko lino lapansi, Mulungu amakhala kuti?

4. Lembani momwe mudamvera mutazindikira kupezeka kwa Mulungu kapenanso kuti Mulungu amachita chinthu china chodalitsa pa moyo wanu. Lembani mwatchutchu kuti mudaatani mutaona izi.

5. Kodi kupezeka ponseponse kwa Mulungu kumathunzitsa mtima wanu motani pamene muli m’mavuto?

6. Mavesi otsatirawa akukutsimikizirani za kupezeka kwa Mulungu. Werengani ndipo muloweze zimene zikugwirizana ndi nyengo zanu kapena kuthandizira wina amene mukumudziwa.

Mulungu alinafe

Eksodo 33:14
Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza

Masalimo 16:11
Mudzandidziwitsa njira ya moyo: Pankhope pano pali chimwemwe chokwanira; Mdzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Masalimo 21:6
Pakuti mumuyikira madalitso kunthawi zonse; mumkonderetsa ndi chimwemwe Pankhope panu.

Masalimo 31:20
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu; Mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.

Masalimo 46:1
Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, Thandizo lopezekeratu m’masautso.

Masalimo 89:15
Odala anthu odziwa liwu la lipenga; Ayenda mkuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Masalimo 139:7-12
Ndidzapita kuti kuzembetsa mzimu wanu?
Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?
Ndikakwera kunka kumwamba muli komweko;
Kapena ndikadzayalira ku Gehena tawonani, muli komweko.
Ndikazitengera mapiko am’bandakucha ndikukhala kumalekero anyanja; kudzakhala komweko dzanja lanu lidzanditsogolera.
Niridzandigwira dzanja lanu lamanja ndipo ndikati, koma mdima undiphimbe, ndikuwunika kondizinga kukhale usiku;
Ungankhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana: Mdima ukunga kuunika.

Yohane 14:3
Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha kuti kumene kuli Ineko, mukakhaleko inunso.

* Ngati imodzi mwamavesi amenewa itha kuthandiza kapena kuthunzitsa mtima wa wina wake amene mukumudziwa, konzani njira yabwino yakuti mugawane kapena kumtumikira.

7. Lembani pemphero lanu lanu kwa Mulungu, lowonetsa kukondwera ndi kupezeka kopotilira kwa Iye pa moyo wanu. Pemphero ili simugawana ndi anzanu panthawi yogawana mawu a m’Baibulo. Lembani pempheroli panopo.

Pemphero
O God, we are overwhelmed by your majesty! How can we ever know the fullness of who You are? You are hidden in light—which cannot be approached. What You are is beyond our ability to express. The Bible plainly tells us that You want us to know You. As we study this next week, open our eyes to see new truths. We worship You. In Jesus’ name, amen.

 

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us