| home >>stonecroft>>mzimu 
            woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo  >>  phunziro 1  
			         
            
             
            KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI?   - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro  #1 
 
 1. Yohane 14:2626Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina 
              langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu 
              zonse zimene ndinanena kwa inu.
  2. Yohane 15:2626Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kucokera 
              kwa Atate, ndiye Mzimu wa coonadi, amene aturuka kwa Atate, Iyeyu 
              adzandicitira Ine umboni.
  Macitidwe 13: 22Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera 
              anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
  Aroma 8:1414Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali 
              ana a Mulungu,
 
 Aroma 8:26
 26Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene 
              tizipempha monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera 
              ndi zobuula zosatheka kuneneka;
  3. 2 Akorinto 1: 21-2221Koma iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Kristu, natidzoza ife, 
              ndiye Mulungu; 22amenenso anatisindikiza cizindikilo, natipatsa 
              cikole ca Mzimu mu mitima yathu.
 4. Yohane 16: 7-117Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke 
              Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati 
              ndipita ndidzamtuma iye kwa inu. 8Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa 
              dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro; 9za 
              macimo, cifukwa sakhulupirira Ine; 10za cilungamo, cifukwa ndinka 
              kwa Atate, ndipo simundionanso; 11za ciweruziro, cifukwa mkuru wa 
              dziko ili lapansi waweruzidwa.
 Yesaya 5:20 20Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene 
              aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene 
              aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
 Jude 1: 14-1614Ndipo kwa iwo, Henoke, wacisanu ndi ciwiri kuyambira kwa Adamu, 
              ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ace zikwi makumi, 
              15kudzacitira onse ciweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa 
              nchito zao zonse zosapembedza, zimene anazicita kosapembedza, ndi 
              pa zolimba zimene ocimwa osapembedza adalankhula pa iye. 16Amenewo 
              ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo 
              pakamwa pao alankhula zazikuruzikuru), akutama anthu cifukwa ca 
              kupindula nako.
 Aroma 6:2323Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya 
              Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.
 Muthu Mzimu wa Mulungu  5. a. Yohane 3: 5-75Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa 
              mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. 6Cobadwa m'thupi 
              cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu. 7Usadabwe 
              cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.
 b. Tito 3: 4-74Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi 
              wathu Mulungu zidaoneka, 5zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, 
              zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa 
              ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
 Yohane 3:1616Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana 
              wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma 
              akhale nao moyo wosatha.
 6. Cibvumbulutso 22:17 17Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani, Ndipo wakumva anene, 
              Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo 
              kwaulere.
 Mulungu ali m'modzi Aroma 8: 9 9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu 
              akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali 
              wace wa Kristu.
 7. 1 Akorinto2:1111Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu 
              uli mwa iye? momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu 
              wa Mulungu.
 Ahebri 9:1414koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda 
              cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima 
              canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?
 Aroma 8: 2, 102Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine 
              ku lamulo la ucimo ndi la imfa.
 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa 
              cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo. 
 |