Project Hope     home >>stonecroft>>mzimu woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1 >> phunziro 2
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #2
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu

Yohane 3: 1-13
1Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda,2Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye, 3Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. 4Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa? 5Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. 6Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu. 7Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano. 8Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, komavsudziwa, kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu. 9Nikodemo anayankha nati kwa iye, Izi zingatheke bwanji? 10Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi? 11Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taeiona; ndipo umboni wathu simuulandira. 12Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba? 13Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma iye wotsikayo kucokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m'Mwambayo.

Yohane 3: 14-21
14Ndipo monga Mose anakweza njoka m'cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa;15kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa iye.
16Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha. 17Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.18Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.19Koma ciweruziro ndi ici, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti nchito zao zinali zoipa. 20Pakuti yense wakucita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe nchito zace.

21Koma wocita coonadi adza kukuunika, kuti nchito zace zionekere kuti zinacitidwa mwa Mulungu.

Macitidwe 1: 1-11
1TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzicita ndi kuziphunzitsa, 2kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha; 3kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zace, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumuwa Mulungu; 4ndipo e posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; 5pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

6Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli? 7Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha. 8Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko. 9Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao. 10Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao; 11amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

Macitidwe 2: 1-13
1Ndipo pakufika tsiku la Penteskoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi.2Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ocokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. 3Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha. 4Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

5Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ocokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo. 6Koma pocitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'cilankhulidwe cace ca iye yekha. 7Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi? 8ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'cilankhulidwe cathu cimene tinabadwa naco? 9Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya; 10m'Frugiya, ndiponso m'Pamfuliya, m'Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo ocokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, 11Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikuru za Mulungu. 12Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzace, Kodi ici nciani? 13koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero.

Macitidwe 2: 14-21
14Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ace, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ici cizindikirike kwa inu, ndi po cherani khutu mau anga. 15Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lacitatulokha la tsiku;16komatu ici ndi cimene cinanenedwa ndi mneneri Yoeli, 17Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse, Ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, Ndi akulu anu adzalota maloto; 18Ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa Ndidzathira ca Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

19Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, Ndi zizindikilo pa dziko lapansi; Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wautsi; 20Dzuwa lidzasanduka mdima, Ndi mweziudzasanduka mwazi, Lisanadze tsiku la Ambuye, Lalikuru ndi loonekera; 21Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.

Macitidwe 2: 36-42
36Pamenepo lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampacika.

37Koma pamene anamva ici, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzacita ciani, amuna inu, abale? 38Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39Pakuti lonjezano 1 liri kwa inu, ndi kwa ana anu, 2 ndi kwa onse akutali, 3 onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana. 40Ndipo ndi mau ena ambiri anacita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.41Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. 42Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

Aroma 8:16
16Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;

Mzimu wa Mulungu mu Chipangano Chakale

1. Genesis 1: 2
2Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa madzi.

Yesaya 40: 12-14
12Ndani wayesa madzi m'dzanja lace, nayesa thambo ndi cikhato, ndi kudzaza pfumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?
13Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lace, ndi kumphunzitsa Iye? 14Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya ciweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?

2. a. Yobu 33: 4
4Mzimu wa Mulungu unandilenga, Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.

b. Ezekieli 36:27
27Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwacita.

c. Mika 3: 8
8Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi ciweruzo, ndi camuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwace, ndi kwa Israyeli cimo lace.

d. 2 Samueli 23: 2
2Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, Ndi mau ace anali pa lilime langa,

Yesaya 11: 2
2ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

Eksodo 31 :3
3ndipo ndamdzaza nd mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso, ndi m'nchito ziri zonse,

Masalmo 51:11
11Musanditaye kundicotsa pamaso panu; Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.

Mzimu Woyera mu chipangano chatsopano

Yohane 14:16
16Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,

Mzimu Woyera mu moyo wa Khristu

3. Luka 4: 16-18
16Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.17Ndipo anapereka kwa iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa, 18Mzimu wa Ambuye uli paine, Cifukwa cace iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, Ndi akhungu kuti apenyenso, Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,

Luka 4: 1
1Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.

Aroma 8:11
11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.

Macitidwe 1: 1-2

1TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzicita ndi kuziphunzitsa, 2kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;

Mateyu 1: 18-20
18Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. 19Koma Yosefe, mwamuna wace, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri, 20Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.

Ntchito Mzimu Woyera 'm mu kulemba Baibulo

4. 2 Petro 1 : 21
21pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

1 Akorinto 2:13
13Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.

Mzimu Woyera mu miyoyo yathu

Agalatiya 3:27
27Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.

Aroma 8:15
15Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,

2 Akorinto 3:18

18Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'cithunzihunzi comweci kucokera kuulenerero kumka kuulemerero, monga ngati kucokera kwa Ambuye Mzimu.

1 Akorinto 3: 16-17
16Kodi simudziwa kuti muli Kacisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? 17Ngati wina aononga kacisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti kacisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

Yohane 6:63
23koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;

 
 

 

Mzimu Woyera uli kuti?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us