|  
               
               Stonecroft Stonecroft Training Mndandanda wa Utatu Malangizo Otsogolera Mavesi a m'BaibuloAdult Stonecroft International The International Team  English YDT Teachings Maphunziro a AnaMalawi Moringa Projects    |  | home >>stonecroft>>mzimu 
            woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo  >>  phunziro 4  >>  phunziro 5             
            
             
             KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI?   - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro  #5 
 
                                                                                     
                  |  |  |  |  
 1 Akorinto 14: 1-40 1Tsatani cikondi; koma funitsitsani mphatsozauzimu, koma koposa 
              kuti mukanenere. 2Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi 
              anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibemunthu akumva; koma mumzimu 
              alankhula zinsinsi.3Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu comangirira 
              ndi colimbikitsa, ndi cosangalatsa, 4Iye wakulankhula lilime, adzimangirira 
              yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo. 5Ndipo ndifuna inu 
              nonse mula'nkhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo 
              wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti 
              Mpingo ukalandire comangirira. 6Koma tsopano, abale, ngati ndidza 
              kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati 
              sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, 
              kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot 7Ngakhale zinthu zopanda 
              moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa 
              maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?8Pakuti 
              ngad Lipenga lipereka mao osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo? 
              9Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika 
              bwanji cimene cilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga. 
              10Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo 
              palibe kanthu kasowa mau. 11Cifukwa cace, ngati sindidziwa mphamvu 
              ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo 
              adzakhala wakunja kwaine. 12Momwemo inunso, popeza muli ofunits 
              its a mphatso zauzimu, funani kuti mukacuruke kukumangirira kwa 
              Mpingo, 13Cifukwa cace wolankhula lilime, apemphere kuti amasule. 
              14Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma 
              cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu. 15Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera 
              ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba 
              ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso. 16Cifukwa ngati udalitsa 
              ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, 
              pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena? 17Pakutitu iwe uyamika 
              bwino, koma winayo samangiriridwa. 18Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula 
              malilime koposa inu nonse; 19koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau 
              asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula 
              mau zikwi m'lilime.
 20Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, 
              koma m'cidziwitso akulu misinkhu. 21Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi 
              anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu 
              awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. 22Cotero 
              malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma 
              kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, 
              koma kwa two amene akhulupira. 23Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse 
              akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo 
              anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka? 
              24Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena 
              wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; 25zobisika 
              za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi, 
              nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa 
              inu. 26Nanga ciani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, 
              ali naco ciphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali 
              naco cimasuliro. Mucite zonse kukumangirira. 27Ngati wina alankhula 
              lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; 
              ndipo mmodzi amasulire. 28Koma ngati palibe womasulira, akhale cete 
              mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.29Ndipo aneneri 
              alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. 30Koma ngati kanthu 
              kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.31Pakuti 
              mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse 
              afulumidwe; 32ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; 33pakuti Mulungu 
              sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse 
              ya oyera mtima. 34Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula, 
              Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena, 35Koma ngati afuna kuphunzirakanthu 
              afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula 
              mu Mpingo. 36Kodi mau a Mulungu anatutuka kwa iw? kapena anafika 
              kwa inu nokha? 37Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti 
              zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye, 38Koma ngati wina 
              akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.39Cifukwa cace; abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse 
              kulankhula malilime. 40Koma zonse zicitike koyenera ndi kolongosoka.
 Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
 Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu Agalatiya 5: 16-2616Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako 
              ca thupi. 17Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu 
              potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna 
              musazicite. 18Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo. 
              19Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba 
              zonyansa, kupembedza mafano, 20nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa 
              mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, 21kuledzera, mcezo, 
              ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti 
              iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 22Koma cipatso 
              ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, 
              kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi 
              palibe lamulo. 24Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba 
              zace, ndi zilakolako zace.
 251 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. 262 Tisakhale 
              odzikuza, outsana, akucitirana njiru. Aroma 6: 1-111Cifukwa cace tidzatani? Tidzakhalabe m'ucimo kodi, kuti cisomo 
              cicuruke?2Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala 
              bwanji cikhalire m'menemo? 3Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse 
              amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace? 
              4Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa 
              muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa 
              Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano. 5Pakuti ngati ife 
              tinakhala olumikizidwa ndi iye m'cifanizidwe ca imfa yace, koteronso 
              tidzakhala m'cifani'Zidwe ca kuuka kwace; 6podziwa ici, kuti umunthu 
              wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo 
              likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo; 7pakuti iye 
              amene anafa anamasulidwa kuucimo. 8Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, 
              tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye; 9podziwa kuti Kristu 
              anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye. 
              10Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye 
              wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. 11Cotero inunso mudziwerengere 
              inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.
 Aroma 6: 12-1912Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa 
              kumvera zofuna zace: 13ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale 
              zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga 
              amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida 
              za cilungamo,14Pakuti ucimo sudzacita ufumu pa inu; popeza simuli 
              a lamulo koma a cisomo.
 15Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma 
              a cisomo? Msatero ai. 16Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka 
              eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace 
              a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena 
              a umvero kulinga kucilungamo? 17Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale 
              mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe 
              aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco; 18ndipo pamene munamasulidwa 
              kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo, 19Ndilankhula manenedwe 
              a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka 
              ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite 
              kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo 
              a cilungamo kuti zicite ciyeretso.  Aroma 6: 20-2320Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira 
              cilungamo. 21Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu 
              zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu 
              izi ciri imfa.
 22Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo 
              a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro 
              cace moyo wosatha. 23Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma 
              mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu 
              Ambuye wathu. Aroma 8: 1-81Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti 
              cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo 
              la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, 
              popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha 
              m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo 
              m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, 
              amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti 
              iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo 
              amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6pakuti cisamaliro 
              ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere. 
              7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja 
              ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene 
              ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
 Aroma 8: 9-179Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu 
              akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali 
              wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu 
              liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo. 
              11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe 
              mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso 
              moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.
 12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala 
              ndi moyo monga mwa thupi; 13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga 
              mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za 
              thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu 
              wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu, 15Pakuti inu simunalandira 
              mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, 
              umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate, 16Mzimu yekha acita umboni 
              pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; 17ndipo ngati 
              ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi 
              olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti 
              tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye. 1. Aroma 5: 8-108Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, 
              kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife. 9Ndipo 
              tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu 
              tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo. 10Pakuti ngati, pokhala 
              ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace, 
              makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo 
              wace.
 2. Aefeso 1: 18-2018ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe 
              inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero 
              wacolowa cace mwa oyera mtima, 19ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu 
              yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba, 
              20imene anacititsa mwa Kristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, 1 namkhazikitsa 
              pa dzanja lace lamanja m'zakumwamba,
 2 Akorinto 13: 44pakuti anapacikidwa m'ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. 
              Pakuti ifenso tiri ofok a mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi 
              ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.
  Aefeso 2:1010Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita 
              nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
 Aroma 8: 9-109Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu 
              akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali 
              wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu 
              liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.
  3. Aefeso 5: 18-2018Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale 
              naye Mzimu,19ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, 
              ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima 
              mwanu; 20ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, 
              m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;
 1 Akorinto 3: 1-31Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu manga ndi auzimu, 
              koma monga athupi, monga makanda mwa Kristu. 2Ndinaiyetsa inu mkaka, 
              si cakudya colimba ai; pakuti simunaeikhoza; ngakhale tsopano lino 
              simucikhoza; pakuti mulinso athupi; 3pakuti, pokhala pali nkhwidzi 
              ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga 
              mwa munthu?
 Macitidwe 9:17; 19b -2017Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja 
              ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu 
              amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa 
              ndi Mzimu Woyera.
 Ndipo anakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena. 
              20Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana 
              wa Mulungu. 4. Aroma 6:1919Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; 
              pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa 
              ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano 
              perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.
 Aroma 12: 11Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, 
              kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa, 
              Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
 1 Petro 4:1919Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa cifuniro ca Mulungu aike 
              moyo wao ndi kucita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.
 Aroma 12: 22Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, 
              mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno 
              ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
 Aroma 8: 1-51Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti 
              cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo 
              la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, 
              popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha 
              m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo 
              m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, 
              amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti 
              iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo 
              amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:
 
 |  |