|  
               
               Stonecroft Stonecroft Training Mndandanda wa Utatu Malangizo Otsogolera Mavesi a m'BaibuloAdult Stonecroft International The International Team  English YDT Teachings Maphunziro a AnaMalawi Moringa Projects    |  | home >>stonecroft>>mzimu 
            woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo  >>  phunziro 5  >>  phunziro 6             
            
             
                      KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI?   - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro  #6 
 
 Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu Aroma 7: 14-2514Pakuti tidziwa kuti cilamulo ciri cauzimu; koma ine ndiri wathupi, 
              wogulitsidwa kapolo wa ucimo. 15Pakuti cimene ndicita sindicidziwa; 
              pakuti sindicita cimene ndifuna, koma cimene ndidana naco, ndicita 
              ici. 16Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, ndibvomerezana naco 
              cilamulo kuti ciri cabwino. 17Ndipo tsopano si ine ndicicita, koma 
              ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. 18Pakuti ndidziwa kuti m'kati 
              mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala cinthu cabwino; pakuti kufuna 
              ndiri nako, koma kucita cabwino sindikupeza. 19Pakuti cabwino cimene 
              ndicifuna, sindicicita; koma coipa cimene sindicifuna, cimeneco 
              ndicicita.20Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, si ndinenso amene 
              ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. 21Ndipo cotero 
              odipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna cabwino, coipa ciriko. 
              22Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi 
              cilamulo ca Mulungu: 23koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana 
              ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la 
              m'ziwalo zanga. 24Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi 
              la imfa iyi? 25Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. 
              Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu; 
              koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo.
 Aroma 8: 1-171Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti 
              cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo 
              la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, 
              popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha 
              m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo 
              m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, 
              amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti 
              iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo 
              amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6pakuti cisamaliro 
              ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere. 
              7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja 
              ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene 
              ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu. 9Koma inu simuli m'thupi 
              ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma 
              ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu. 10Ndipo 
              ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa 
              ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo. 11Koma ngati 
              Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye 
              amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu 
              akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.
 12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala 
              ndi moyo monga mwa thupi; 13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga 
              mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za 
              thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu 
              wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu, 15Pakuti inu simunalandira 
              mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, 
              umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate, 16Mzimu yekha acita umboni 
              pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; 17ndipo ngati 
              ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi 
              olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti 
              tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye. Akolose 3: 1-171Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba, 
              kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu. 2Lingalirani 
              zakumwamba osati za padziko ai. 3Pakuti munafa, ndipo moyo wanu 
              wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu, 4Pamene Kristu adzaoneka, 
              ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.
 5Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso 
              ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza 
              mafano;6cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;7zimene 
              munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo, 
              8Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, 
              mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu: 9musamanamizana wina ndi 
              mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,10ndipo 
              munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco 
              cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;11pamene 
              palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, 
              Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse. 12Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima 
              ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, 
              kuleza mtima; 13kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana 
              eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye 
              anakhululukira inu, teroni inunso;14koma koposa izi zonse khalani 
              naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu. 15Ndipo mtendere 
              wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi 
              limodzi; ndipo khalani akuyamika. 16Mau a Knstu akhalitse mwa inu 
              cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni 
              okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira 
              Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu. 17Ndipo ciri conse mukacicita 
              m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi 
              kuyamika Mulungu Atate mwa iye. Aroma 12: 1-81Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, 
              kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa, 
              Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. 2Ndipo musafanizidwe ndi 
              makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso 
              kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, 
              cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
 3Pakuti ndi cisomo capatsidwa kwa ine, ndiuza munthu ali yense 
              wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize 
              modziletsa yekha, monga, Mulungu anagawira kwa munthu ali yense 
              muyeso wa cikhulupiriro, 4Pakuti monga m'thupi limodzi tiri nazo 
              ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo siziri nayo nchito imodzimodzi; 
              5comweco ife, ndife ambiri, tiri thupi limodzi mwa Kristu, ndi ziwalo 
              zinzace, wina ndi wina. 6Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, 
              monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, 
              tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;7kapenayakutumikira, 
              tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; 
              8kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi 
              mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, 
              acite ndi kukondwa mtima. Aroma 12: 9-219Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana 
              naco cabwino. 10M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane 
              ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu; 
              11musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani 
              Ambuye; 12kondwerani m'ciyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani 
              cilimbikire m'kupemphera,13Patsani zosowa oyera mtima; cerezani 
              aulendo. 14Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. 
              15Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. 16Mukhale ndi 
              mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma 
              phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. 
              17Musabwezere munthu ali yense coipa cosinthana ndi coipa. Ganiziranitu 
              zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. 18Ngati nkutheka, monga momwe 
              mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. 19Musabwezere coipa, 
              okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera 
              kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. 20Koma ngati mdani wako 
              akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero 
              udzaunjika makala a mota pamutu pace. 21Musagonje kwa coipa, koma 
              ndi cabwino genietsani coipa.
 Aroma 15: 1-131Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofoka za opanda 
              mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. 2Yense wa ife akondweretse 
              mnzace, kumcitira zabwino, zakumlimbikitsa. 3Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa 
              yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe 
              Inagwa pa Ine,4Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, 
              kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo. 
              5Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale 
              ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu; 6kuti nonse 
              pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye 
              wathu Yesu Kristu. 7Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso 
              Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.
 8Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa 
              ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa 
              makolo, 9ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa 
              ca cifundo; monga kwalembedwa,Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu,
 Ndidzayimbira dzina lanu.
 10Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.
 11Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; Ndipo anthu onse 
              amtamande.
 12Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Jese, Ndi iye amene aukira 
              kucita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.
 13Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi 
              mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu 
              ya Mzimu Woyera.
 3. Yohane15: 1-8 1Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. 2Nthambi 
              iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala 
              cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka. 3Mwakhala okonzeka 
              tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu, 4Khalani mwa 
              Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa 
              yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala 
              mwa Ine. 5Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa 
              Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda 
              Ine simungathe kucita kanthu. 6Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika 
              kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, 
              nazitentha. 7Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, 
              pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu. 8Mwa 
              ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo 
              mudzakhala akuphunzira anga.
 Kulepheretsa Mzimu Woyera 5. Macitidwe 7:5151 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu 
              Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.
 1 Atesalonika 5: 19-2019Musazime Mzimuyo;
 20Musanyoze maaenero;
 Yesaya 63:1010Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa cisoni mzimu wace woyera, cifukwa 
              cace Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
 Macitidwe 5: 33Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa 
              ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?
 6. Afilipi 4: 6-76Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, 
              pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. 7Ndipo 
              mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima 
              yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.
  Aroma2:1515popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, 
              ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo 
              ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;
 1 Samueli 10: 77Ndipo zitakufikirani zizindikilo izi mudzacita monga mudzaona pocita, 
              pakuti Mulungu ali nanu.
 2 Timoteo 3:1616Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, 
              citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:
 7. 1 Yohane 3 : 11Taonani, cikondico Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu; 
              ndipo tiri ife otere. Mwa ici dziko lapansi silizindikira ife, popeza 
              silimzindikira iye.
  Yohane 15 :1515Sindichanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye wace 
              acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva kwa 
              Atate wanga ndakudziwitsani.
  Afilipi 3 :20-2120Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; z kucokera komwenso tilindirira 
              Mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu; 21amene adzasanduliza thupi lathu 
              lopepulidwa, lifanane nalo thupi lace la ulemerero, monga mwa macitidwe 
              amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.
  Aefeso 3 :1212amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa 
              cikhulupiriro ca pa iye.
 1 Akorinto 6 :19-2019Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, 
              amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala 
              a inu nokha. 20Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa 
              cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
 Yakobo 1: 2-52Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero 
              a mitundu mitundu; 3pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro 
              canu cicita cipiriro.4Koma cipiriro cikhale nayo nchito yace yangwiro, 
              kuti mukakhale angwiro ndi opanda cirema, osasowa kanthu konse.
 5Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa 
              kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,
 Yauzimu  8. b. Aefeso 6: 10-1810Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu 
              yace.11Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika 
              pokana macenjerero a mdierekezi. 12Cifukwa kuti kulimbana kwathu 
              sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, 
              ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a 
              coipa m'zakumwamba. 13Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, 
              kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita 
              zonse, mudzacirimika. 14Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira 
              m'cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo; 
              15ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino 
              wa mtendere; 16koposa zonse mutadzitengeranso cikopa ca cikhulupiriro, 
              cimene mudzakhoza kuzima naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo. 
              17Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo 
              Mau a Mulungu; 18mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi 
              yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera 
              oyera mtima onse,
  9. Yakobo 4: 7-87Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani 
              inu. 8Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani 
              m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
 1 Petro 5: 8-108Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango 
              wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: 9ameneyo mumkanize 
              okhazikika m'cikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zirimkukwaniridwa 
              pa abale anu ali m'dziko.10Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene 
              adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa 
              kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa, 
              adzalimbikitsa inu.
 Aefeso 6:1313Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima 
              citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.
 Aefeso 4: 22-2722kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, 
              wobvunda potsata zilakolako za cinyengo; 23koma kuti 1 mukonzeke, 
              mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, 242 nimubvale munthu watsopano, 
              amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca 
              coonadi.
 25Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 
              4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace. 265 Kwiyani, koma musacimwe; 
              dzuwa lisalowe muli cikwiyire, 27ndiponso 6 musampatse malo mdierekezi.
  10. 2 Akorinto 10: 3-53Pakuti pakuyendayenda m'thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi, 
              4(pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa 
              Mulungu zakupasula malinga); 5ndi kugwetsa matsutsano, ndi cokwezeka 
              conse cimene cidzikweza pokana ddziwitso ca Mulungu, ndi kugonjetsa 
              ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu;
 2 Akorinto 6: 77m'mau a coonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa camuna ca cilungamo 
              kulamanja ndi kulamanzere,
 Aefeso 6:1717Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo 
              Mau a Mulungu;
 Masalmo 50:1515Ndipo undiitane tsiku la cisautso:
 Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.
 1 Yohane 4: 44Inu ndinu ocokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti iye 
              wakukhah mwa inu aposa iye wakukhala m'dzi ko lapansi. Iwo ndiwo 
              ocoken m'dziko lapansi;
 11. a. 2 Petro 3:18 18Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi 
              Yesu vistu; kwa iye kukhale uleme'ero, tsopano ndi nthawi zonse. 
              Amen.
  12. Agalatiya 5:1616Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako 
              ca thupi.
   |  |