Project Hope     home >>stonecroft>>mzimu woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 3 >> phunziro 4
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #4
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu

1 Akorinto 13: 1-13
1Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. 2Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe. 3Ndipo ndingakhale ndipereka cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu ai. 4Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza, 5sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa; 6sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;7cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse. 8Cikondi sicitha nthawizonse, koma kapena zonenera zidzakhala cabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala cabe.9Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. 10Koma pamene cangwiro cafika, tsono camderamdera cidzakhalacabe. 11Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa cabe zacibwana. 12Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati cimbuuzi; koma R pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. 13Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.

Aroma 8: 1-8
1Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere. 7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

Aroma 8: 9-17
9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo. 11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.

12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi; 13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu, 15Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate, 16Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; 17ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.

1 Akorinto 12: 1-11
1Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.2Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa. 3Cifukwa cace ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yew ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

4Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo. 5Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo. 6Ndipo pali macitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakucita zinthu zonse mwa onse. 7Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao. 8Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: 9kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo; 10ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime. 11Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

1 Yohane 4: 7-21
7Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu, 8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi. 9Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye. 10Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu. 11Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo 12Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife; 13m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace. 14Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu. 16Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye. 17M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.18Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.19Tikonda ife, cifukwa anayamba iye kutikonda. 20Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wace, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale ware amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona. 21Ndipo lamulo ili tiri nalo locokera kwa iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wace.

Galates 5: 16-26
16Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi. 17Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite. 18Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo. 19Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, 20nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, 21kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo. 24Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace.

251 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. 262 Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.

1 Petro 5: 14b
Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Kristu.

1 Yohane 1: 9
9Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse

1. Agalatiya 5: 22-23
22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

1 Akorinto 13:13
13Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.

Chipatso cha Mzimu

2. Mateyu 22: 34-40
34Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.35Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati, 36Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo? 37Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. 38Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba. 39Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. 40Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri.

Kukonda

3. a. Akolose 3:19
19Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.

b. Luka 6: 27-28
27Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; citirani zabwino iwo akuda inu, 28dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akucitira inu cipongwe.

c. Tito 2: 3-4
3Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa naco cikondi ca pavinyo, akuphunzitsa zokoma; 4kuti akalangize akazi ang one akonde amuna ao, akonde ana ao,

d. Yohane 13: 34-35
34Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace. 351 Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.

e. Mateyu 22:39
39Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

f. Aefeso 5: 2
2ndipo yendani m'cikondi monganso Kristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, copereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale pfungo lonunkhira bwino.

Aroma 12: 9-10
9Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana naco cabwino. 10M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;

Aroma 5: 5
5ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Chimwemwe

Afilipi 4: 4
4Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

Mtendere

Afilipi 4: 6-7
6Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. 7Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.

Yohane 14:27
274 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.

Chipiriro

4. Aroma 15: 5
5Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;

Mtima

5. Akolose 3:12
12Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

Ubwino

6. Aefeso 2:10
10Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Kukhulupirika

Luka 16: 10-12
10Iye amene akhulupirika m'cacing'onong'ono alinso wokhulupirika m'cacikuru; ndipo iye amene ali wosalungama m'cacing'onong'ono alinso wosalungama m'cacikuru. 11Cifukwa cace ngati simunakhala okhulupirika m'cuma ca cosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi cuma coona? 12Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zace za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

7. 2 Atesalonika 3: 3
3Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

Kudzichepetsa

Afilipi 2: 3-8
3musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini; 4munthu yense asapenyerere zace za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzaceo 5Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, 6ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,7koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu; 8ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

Kudzigwira

Tito 2: 11-12
11Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse, 12ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

Afilipi 1:11
11odzala nacocipatso ca cilungamo cimene ciri mwa Yesu Kristu, kucitira Mulungu ulemerero ndi ciyamiko.

Mphatso za mzimu

Agalatiya 5:22-23
22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

1 Akorinto 12:11
11Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

1 Petro 4:10
10monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a cisomo ca mitundu mitundu ca Mulungu;

8. 1 Petro 4:10
10monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a cisomo ca mitundu mitundu ca Mulungu;

9. 1 Akorinto 12: 8-10
8Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: 9kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo;

Aroma 12: 6-8
6Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;7kapenayakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;

1 Akorinto 12:11
11Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

 

 
 

 

Mzimu Woyera uli kuti?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us