Project Hope     home >>stonecroft>>mzimu woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 2 >> phunziro 3
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #3
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu

Yohane 14: 1-14
1Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.2M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. 3Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. 4Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace. 5Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? 6Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

7Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye. 8Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira. 9Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate? 10Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.11Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe. 12Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate. 13Ndipo cimene ciri conse mukafunse m'dzina langa, ndidzacicita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.14Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzacita.

Yohane14: 15-31
15Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.
16Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse, 17ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu. 18Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu. 19Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo. 20Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. 21Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.

Yohane 15: 1-17
1Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. 2Nthambi iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka. 3Mwakhala okonzeka tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu, 4Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. 5Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kucita kanthu. 6Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha. 7Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu. 8Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga. 9Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga. 10Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace. 11Izi ndalankhula ndi inu, kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cidzale. 12Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzace, monga ndakonda inu. 13Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace. 14Muli abwenzianga inu, ngati muzicita zimene ndikulamulirani inu.

15Sindichanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye wace acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. 16Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala cipatso, ndi kuti cipatso canu cikhale; kuti cimene ciri conse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu. 17Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzace.

Yohane 15: 18-27
18Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.19Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zace za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, cifukwa ca ici likudani inu. 20Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.21Koma izi zonse adzakucitirani cifukwa ca dzina langa, cifukwa sadziwa wondituma Ine. 22Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo cimo; koma tsopano alibe cowiringula pa macimo ao. 23Iye wondida Ine, adanso Atate wanga. 24Sindikadacita mwa iwo nchito zosacita wina, sakadakhala nalo cimo; koma tsopano anaona, nada: Ine ndi Atate wanganso, 25Koma citero, kuti mau olembedwa m'cilamulo cao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda cifukwa.

26Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kucokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa coonadi, amene aturuka kwa Atate, Iyeyu adzandicitira Ine umboni. 27Ndipo inunso mucita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira ciyambi.

Yohane 16: 1-15
1Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe. 2Adzakuturutsani m'masunagoge; koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu, 3Ndipo izi adzacita, cifukwa sanadziwa Atate, kapena Ine.4Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira paciyambi, cifukwa ndinali pamodzi ndi inu. 5Koma tsopano ndimuka kwa iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti? 6Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu.

7Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu. 8Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro; 9za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine; 10za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso; 11za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa. 12Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. 13Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani. 14Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu. 15Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; cifukwa cace ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

Yohane 16: 16-33
16Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine. 17Mwa akuphunzira ace tsono anati wina ndi mnzace, ici nciani cimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, cifukwa ndimuka kwa Atate? 18Cifukwa cace ananena, ici nciani cimene anena, Kanthawi? Sitidziwa cimene alankhula.19Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzace za ici, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine? 20Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzacita cisoni inu, koma cisoni canu cidzasandulika cimwemwe. 21Mkazi pamene akuti abale ali naco cisoni, cifukwa yafika nthawi yace; koma pamene wabala mwana, sakumbukilanso kusaukako, cifukwa ca cimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi. 22Ndipo inu tsono muli naco cisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzacotsa kwa inu cimwemwe canu. 23Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa. 24Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.
25Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate. 26Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate; 27pakuti Atate yekha akonda inu, cifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinaturuka kwa Atate.28Ndinaturuka mwa Atate, ndipo ndadza ku dziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.

29Akuphunzira ace ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena ciphiphiritso, 30Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ici tikhulupirira kuti munaturuka kwa Mulungu. 31Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano? 32Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zace za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, cifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine, 33Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.

Mzimu Woyera mu miyoyo yathu

1. a. 1 Yohane 2:27
27Ndipo inu, 8 kudzoza kumene munalandira kucokera kwa iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma 9 monga kudzoza kwace kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye.

b. Yohane 16: 13-14
13Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani. 14Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

c. Aroma 8:14
14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,

d. Agalatiya 5: 22-23
22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

e. Macitidwe 1: 8
8Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.

Pemphero

Marko 1:35
35Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko.

2. Macitidwe 8:26
26Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwela, kutsata njira yotsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya cipululu.

1 Yohane 5: 14-15
14Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera; 15ndipo ngati tidziwa kuti atimvera ciri conse ticipempha, tidziwa kuti tiri nazo izi tazipempha kwa iye.

3. a. 1 Atesalonika 5:17
17Pempherani kosaleka;

4. a. Mateyu 6: 5-6
5Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 6Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.

b. Masalmo 55:17
17Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, Ndipo adzamva mau anga.

Kuwerenga Baibulo

1 Akorinto 1:18
18Pakuti mau a mtanda ali ndithu cinthu copusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tirikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.

Kumvera

6. Yakobo 1: 22-25
22Khalani akucita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. 23Pakuti ngati munthu ali wakumva mau wosati wakucita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yace ya cibadwidwe cace m'kalirole; 24pakuti wadziyang'anira yekha nacoka, naiwala pompaja nali wotani.25Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero cipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakucita nchito, adzakhala wodala m'kucita kwace.

Agalatiya 5:17
17Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.

1 Akorinto 10:13
13Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

7. Aefeso 4: 25-32
25Mwa ici, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzace; pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace. 26 Kwiyani, koma musacimwe; dzuwa lisalowe muli cikwiyire, 27ndiponso musampatse malo mdierekezi. 28Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse nchito, nagwire nchito yokoma ndi manja ace, kuti akhale naco cakucereza wosowa. 29 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva. 30Ndipo musamvetse cisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe. 31 Ciwawo conse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi ciwawa, ndi mwano zicotsedwe kwa inu, ndiponso coipa conse.32Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzace, a mtima wacifundo,

1 Akorinto 6: 19-20
19Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. 20Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

8. Agalatiya 5:16
16Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.

 

 
 

 

Mzimu Woyera uli kuti?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us